Tili ndi masomphenya okonza mphamvu za magetsi patokha — yatero kampani ya Illovo

Advertisement

Kampani yopanga shuga m’dziko muno ya Illovo yalengeza kuti ili ndi masomphenya okonza mphamvu za magetsi payokha kuti ichepetse ndalama zimene kampaniyi imaluza kulipira magetsi ku ESCOM.

Mkulu wa kampaniyi, Lekani Katandula, ndiye anayankhula izi lero mu mzinda wa Blantyre pamene anali ndi nkumano ndi anthu ena amene amathandizira kuyendetsa ntchito za kampaniyi.

“Masomphenya wa anakhazikitsidwa chaka chatha koma chifukwa cha zovuta zina kunali kovuta kuti akwanilitsidwe,” antero a Katandula.

Ngakhale izi zili chomwechi, kampaniyi inapeza phindu lochepa la ndalama zokwana 25 biliyoni mu theka la chaka chino pamene theka la chaka chatha inapeza 33.7 biliyoni.

Advertisement