Musalowetse ndale – wachenjeza Bushiri

Advertisement
Shepherd Bushiri Malawi

Mtsogoleri wa mpingo wa ECG – Jesus Nation, Shepherd Bushiri, wachenjeza anthu omwe akulowetsa ndale pa ntchito yake yogawa chimanga kwa anthu omwe akhudzidwa ndi njala kuti asiye ponena kuti iye akupanga izi kungofuna kuthandiza.

Bushiri wayankhula izi Loweluka pa 17 February, 2024 pomwe anali m’boma la Thyolo komwe amapitiliza ntchito yogawa chimanga yomwe wayikhazikitsa posachedwapa.

Pa mwambowu, Bushiri anadandaula kuti pali anthu ena omwe akufuna kulowetsa ndale pa pologalamu yogawa chimangayi ndipo wachenjeza kuti izi zitheretu ponena kuti iye si munthu wa ndale.

“Ndimafuna ndichenjeze onse omwe akufuna kulowetsa ndale pa pologalamu yogawa chimanga. Chonde siyani zimenezo, ine sine munthu wa ndale. Ine ndimangoika dziko langa patsogolo.  Izi siza ndale chonde,” watelo Bushiri.

Iye walimbikitsa anthu mdziko muno kuti atenge nawo gawo kuthana ndi njala yomwe yakhudza madera ambiri, ponena kuti kugawa chimanga sizimatengera kuti uli ndi zinthu za mbiri kapena zochepa.

M’boma la Thyolo, anthu osachepera 1500 alandira aliyese thumba la chimanga zomwe mfumu yaikulu Nchiramwera ayamikira ponena kuti anthu kudera lawo akuvutika kwambiri ndi njala.

“Ife kwathu ndikungothokoza. Tikuti zikomo kwambiri Bushiri chifukwa chotiganizira ife kuno. Kunena zoona, anthu kunoku ali pa mavuto adzaoneni pa nkhani ya chakudya ndipo thandizo ili litikankha kwa masiku angapo,” yatelo mfumu yaikulu Nchiramwera.

Posachedwapa, Bushiri anakhazikitsa ntchito yogawa chimanga chochuluka matani 17,000 chomwe ndi cha ndalama zosachepera 14 biliyoni kwacha ndipo lamulungu pa 18 February, 2024, akuyembekezeka kukagawa chimangachi m’boma la Mulanje.

Advertisement