Professor Ngeyi Kanyongolo awasankha kukhala wachiwiri kwa wamkulu wa Catholic University

Advertisement
Ngeyi Kanyongolo is the new vice chancellor of Catholic University in Malawi

Bungwe la mabishopu achikatolika la Episcopal Conference of Malawi (ECM) lasankha katswiri pankhani ya zamalamulo Professor Ngeyi Kanyongolo kukhala wachiwiri kwa wamkulu wa Catholic University.

Bungwe la ECM lalengeza zakusankhidwa kwa a Kanyongolo kudzera muchikalata chomwe bungweli latulutsa.

Chikalatachi chomwe wasayinira ndi wapampando wa bungwe la ECM Archbishop George Desmond Tambala chati asankha Prof Kanyongolo chifukwa alindi zonse zowayenereza monga pamaphunziro apamwamba komanso kutengera ndintchito zomwe akhala akugwira mbuyomu.

Professor Ngeyi Ruth Kanyongolo ali ndi PhD yomwe adayipeza ku University ya Warwick chaka cha 2007, masters degree yomwe adayipeza ku University yaku London chaka cha 1997, komanso ali ndi bachelor’s degree yomwe adayipe byza ku University of Malawi chaka cha 1991.

Kupatula kukhala Mphunzitsi wadza malamulo ku University of Malawi, Prof Kanyongolo akhalaponso maudindo osiyanasiyana monga mkulu wa bodi ya Standard Bank, ya Airtel Malawi ndi ya Old Mutual. Adakhalaponso wachiwiri kwa mtsogoleri wa Malawi Law Society kungotchulapo zochepa.

Iwo adapuma ntchito ngati m’phunzitsi wadza malamulo ku University ya Malawi mu chaka cha 2023.

Advertisement