Mboni zambali ya Boma zatsiliza kuperekera umboni pamulandu wa a Bon Kalindo

Advertisement

Mboni zisanu zambali ya Boma zatsiliza kuperekera umboni pamulandu wamkulu wa Bungwe la Malawi First a Bon Kalindo omwe akuwayimba mulandu owaganizira kuti adayambitsa zipolowe potsatira ziwonetsero zomwe adachititsa pa 23 November mu mzinda wa Zomba.

Zina mwambonizo ndi apolisi anayi omwe ndi Stella Likukuta, Harry Dongolosi, Inspector Gauti, komanso Assistant Superintendent Isaac Mdala.

Onsewa ndi ofudzufuza milandu ya upandu ku nthammbi ya a Police ndipo winanso yemwe waperekera nawo umboni pankhani yomweyi ndiyemwe amagwira ntchito kumalo ogulitsira zokumwa a Kangaroo ku Chinamwali Township a Christopher Ndanga.

A Ndanga adauza bwalo kuti tsiku lomwe kudachitika ziwonetsero anthu ena omwe sakudziwika adabwera masana cha m’ma 2 koloko kudzaba zokumwa zomwe ndi zandalama pafupi fupi 8.5 million kwacha.

Poyankhula ndi Malawi24, Loya yemwe akuyimira a Bon Kalindo pamulanduwu a Timothy Chirwa adati gawo loyamba lamulanduwu latha akungodikilira bwalo kuti liwunikire zonse zomwe mboni zapereka ndipo lidzagamule ngati a Bon Kalindo alindi mulandu okuti ayankhe kapena ayi pa 21 February.

Yemwe akuyimira Boma pamulanduwu Superintendent Josephine Chigawa adati ndiwokhutira ndi momwe mboni zawo zaperekera umboni.

Yemwe akudzenga mulanduwu Principal Resident Magistrate Martin Chipofya wayamba wayimitsa mulanduwu mpaka pa 21 February 2 koloko masana kuti adzagamule ngati kuti a Kalindo alindi mulandu okuti ayankhe kapena ayi.

Pamenepa Principal Resident Magistrate Chipofya waudza oyimira Boma pamulanduwu kuti apereke ma submission awo pokutha kwa masiku asanu ndi awiri (7) kwa omwe akuyimira a Bon Kalindo komanso waudza omwe akuyimira a Kalindo kuti akhale atapereka ma submission awo kumbali yomwe ikuyimira Boma pofika pa 14 February mwezi wa mawa.

Advertisement