Achinyamata 140 akupita ku Israel mawa


Israel Malawi

Achinyamata okwana 140 akuyembekezeka kunyamuka m’dziko muno mawa kupita ku Israel komwe akukagwira ntchito ku minda.

Achinyamatawa omwe afika kale Ku Kamuzu International Airport akhala akunyamuka m’bandakucha wa lachitatu.

Polankhula ndi Malawi24, mkulu wa kampani yomwe ikutumiza achinyamata yotchedwa Arava Farmers Agency a Justice Kangulu anena kuti achinyamatawa akukagwira ntchito zosiyanasiyana ku minda ya ku Israel.

Iye anaonjezela kunena kuti onse akuwonetsa kuti ali okonzeka komanso osangalala kuti apeza mwayi okagwira ntchito Ku Israel komwe azikalandira ndalama zankhaninkhani.

Pakali pano, achinyamata oposa 400 ali kale ku Israel komwe akugwila ntchito mu minda ya kumeneko.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.