Buluzi wa ize adapanidwa mchitseko: Ena ku Luanar yauma kamba ndi nyani m’mayeso


Luanar

Sukulu ya ukachenjede ya Luanar yapereka zilango kwa ophunzira okwana 19 kamba kopezeka olakwa pa mlandu owonera mayeso ndipo atatu mwa ophunzirawa awachotsa sukulu.

Ophunzira pamene khumi ndi anayi ayimitsidwa sukulu kwa zaka ziwili, ena chaka chimodzi pamene awili alandira chenjezo.

Malingana ndi kalata yomwe sukuluyi yatulutsa, ophunzirawa alandira zilangozi kamba kopezeka ndi lamya za m’manja mchipinda cholembera mayeso, kupezeka ndima likasa, kusinthana notsi, komanso kulemba mayeso popanda kulembetsa.

Mmasiku apitawo, sukulu ya ukachenjede ya Malawi Business of Applied Science (MUBAS) idachotsanso ophunzira ena kamba kowonera mayeso ndipo nayonso University of Malawi (UNIMA) idalengezanso kuti yapereka zilango kwa ophunzira ochita mchitidwewu.

Vuto lakuonera mayeso likukura msukulu za ukachenjedezi kamba koti ambili amatangwanika ndi zisangalalo mmalo mopeza nthawi yomawerenga ndipo pamapeto pake amapeza kuti kuonera ndiyo njira yabwino.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.