Ogwira ntchito anayi pa kampani ya ETG awanjata kamba kogwinya feteleza

Advertisement
Three suspects who were stealing from farmers

Ogwira ntchito anayi apa kampani yogulitsa zipangizo za ulimi ya Export Trading Group (ETG) awanjata ndikuwaponya mchitokosi cha apolisi ku Dowa kamba kowaganizira kuti adakwangwanula m’matumba afetereza pa kampanipo.

Anthu anayi oganizilidwawa ndi a Sigele Selemani azaka 25, a Tionge Mazibuko azaka 37, a Gabriel Kayange azaka 31 komanso Fabiano Banda azaka 26 zakubadwa.

Nkhani yonse ikuti  sabata latha pa 20, yemwe ndi mkulu wakampaniyi mchigawo chapakati a Ivy Sinda anali paulendo oyendera malo ena ogulitsira zipangizo za ulimi akampaniyi ndicholinga chofuna kuwerengera katundu m’malowa koma anatutumuka ndizomwe ogwira ntchitowa anali kuchita pa Dowa.

Pa 24 January, a Sinda anayenderanso pamalo ogulitsira zipangizozi pofuna kupitiliza ntchito yowelengera zipangizo za ulimizi koma nawo a Malawi Bureau of Standards anafikanso pamalopo.

Ogwira ntchitowa anadziwitsa a Sinda ponena kuti matumba a feteleza omwe akugulitsa pa malopa ndi osakwanira makilogalamu makumi asanu. Izi zinapangitsa kuti ayeze matumbawo ndipo atayeza anapeza kuti matumba 15 ndi omwe samakwana makilogalamu 50.

Akuluakulu pa kampaniyi anatsina khutu apolisi pa nkhaniyi ndipo apolisi sanachedwe koma kuchita kafukufuku pa zankhaniyi ndikumanga oganizilidwawa. Apa ogwira ntchito anayiwa anavomera kuti amapunguladi fetelezayu m’matumbamo.

Pakadali pano, ogwira ntchito anayiwa akuyembekezeka kukaonekela ku bwalo la milandu ndikuyankha mulandu wakuba pa malo a ntchito.

Advertisement