Boma lati ligwira ntchito limodzi ndi mnyamata wakonza magetsi ku Dowa

Advertisement
A boy in Dowa has produced electricity for his communitu

Boma kudzera mwa nduna yoona zamagetsi mdziko muno a Ibrahim matola, lalonjeza kuti lithandiza nyamata uja wakonza magetsi oyendera madzi ndi mpweya ku Dowa kufikira masomphenya ake oyika magetsi pa sukulu ya Kongwe 2 komanso nyumba za m’mudzi mwake atakwanilitsidwa.

Nduna yoona za magetsi mdziko muno a Ibrahim Matola ndi omwe ayankhula izi lero la chisanu pomwe ndunayi inamuyendera Enerst Andrew yemwe wakonza magetsiwa kwawo ku Dowa m’mudzi wa Chinguwo, kwa mfumu yaikulu Chiwere.

A Matola anati sangamukakamize mnyamatayu kuti abwelelenso mkalasi kamba koti nyamatayu sukulu adasiya ndikare. Kotero a Matola anati boma limuthandiza kuti nyamatayu akwanilitse masomphenya ake oyika magetsi pasukulu ya pulayimale komanso m’mudzi mwawo.

Koma mnyamatayu wapempha ndunayi kuti imuthandize pomugulira nthambo zamagetsi ndi cholinga choti akwanilitse kupala magetsiwa.

Ndunayi yayendera mnyamatayu kutsatira masiku apitawo nyamatayu wakhala akuyikidwa m’masamba amchezo kuonetsa luso lake la pamwambali.

Advertisement