
Bwalo la milandu munzinda wa Lilongwe lalamura kuti Prophet Shepherd Bushiri komanso mkazi wake Mary, atumizidwe mdziko la South Africa kuti akayankhe milandu yokhudza ndalama komanso yogwililira yomwe akuganizilidwa.
Koma awiri ati akachita apilo chigamulochi. Popeleka chigamulochi, Senior Resident Magistrate Madalitso Chimwaza adalamula kuti awiriwa akasungidwe kaye kundende podikira kuwatumiza ku South Africa kukayankha milandu yomwe akuwaganizira kuti adapalamurayi.
Koma Bushiri adati ndiwosakhutira ndi chigamulochi ndipo kudzera mwa owayimilira awo omwe ndikuphatikizapo Wapona Kita, adauza khothi kuti akachita apilo chigamulochi ndipo anapempha kuti chigamulochi chiyimitsidwe kaye.
Popeleka chigamulo chake pa pempholi, Chimwaza adavomera kuti chigamulo chake choti awiriwa atumizidwe achiyimike kaye kwa masiku 30 pofuna kupereka mpata kuti Bushiri akadandaule za nkhaniyi ku bwalo lalikulu.
Bushiri pamodzi ndi mkazi wake Mary adathawa m’dziko la South Africa mu 2020 ndipo sizimadziwikabe mpaka pano momwe adayendera kuti adzafike kuno ku Malawi. Ngati angatumizidwe m’dziko la South Africa, awiriwa akayeneranso kuyankha mlandu wothawa belo.