Chakwera aboola mtambo lero wa ku DRC


Malawi President Lazarus Chakwera

Mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera akuyembekezeka kuboola mtambo lero pa ulendo opita mdziko la Democratic Republic of Congo (DRC).

A Chakwera akukawonelera mwambo olumbilitsa mtsogoleri wadzikolo a Felix Tshisekedi Tshilombo yemwe wangosankhidwanso  kumene komanso akukakambilana ndi a Tshisekedi zokhudzana ndi asilikali a Malawi omwe akugwira ntchito yosungitsa bata ku DRC.

Malingana ndi kalata yomwe yatulutsa ndi unduna woona za ubale pakati padziko lino ndi mayiko akunja, a Chakwera analibe malingaliro opita ku DRC koma ayenda chifukwa chakuti ayitanidwa ndi a Tshisekedi.

Mtsogoleri wa dziko linoyu anyamuka 11 koloko m’mawa uno kudzera pa bwalo la ndege la Chileka munzinda wa Blantyre ndipo akuyembeka kudzabwelera kuno ku Malawi lamulungu.

Aka nkoyamba a Lazarus Chakwera kuboola mtambo kutuluka mdziko lino chilengezeleni kuti wayimitsa maulendo ake mu November chaka chatha. A Chakwera adanena  kuti adzayambilanso kuyenda mu April  chaka chino ndicholinga chakuti chuma cha boma chisaonengeke.

Sponsored

Wolemba: Ben Bongololo

One comment on “Chakwera aboola mtambo lero wa ku DRC

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading