Nzika ya dziko lino a Eddie Longwe omwe amakhala m’dziko la Kuwait ati ali ndi chidwi chopikisana nawo pa zisankho za mtsogoleri wadziko lino zomwe zikuyembekezeka kuchitika chaka chamawa.
A Longwe auza Malawi24 kuti iwo ndiwokonzeka kuombola amalawi omwe pakadali pano akukumana ndimavuto osiyanasiyana mu ulamuliro wa presidenti Lazarus Chakwera.
Iwo ati ali ndinfundo zikuluzikulu zingapo zomwe akuti ndizothandiza kutukula dziko lino komaso miyoyo ya amalawi.
Zina mwamfundozi ndimonga kuthana ndi katangale, kulimbikitsa nkhani za ulimi ndikuti dziko lino likhale ndichakudya chokwanira, kulimbikitsa ulamuliro wabwino, kulimbitsa chitetezo cha dziko komanso kutukula ntchito za umoyo m’magawo osiyanasiyana.
“Pali zambiri zomwe ndakonzekera kuwachitira a malawi anzanga. Azuzika kokwana ndipo nthawi yoti awomboledwe yakwana,” watero Longwe.
Kotero iye wapempha anthu kuti adzamuvotere mwa unyinji kuti masomphenya ake azakwanilitsidwe maka ofuna kutukula dziko lino.
Longwe anabadwira ndikukulira mchigawo chakumpoto kwadziko lino. Bambo ake amachokera m’boma la Nkhotakota pomwe mayi ake amachoka m’boma la Mzimba.
Kunkhani zamaphunziro, Longwe ali ndi digli ya za business komaso diploma yokhudza makompyuta.