Pita koma usakachimweso: Wanderers ayiletsa kusewera mpira ku Malawi koma isewerabe

Advertisement
Malawi Football

Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yapulumukira dzenje lokumbakumba pomwe bungwe loyendetsa mpira mdziko muno la FAM lauza timuyi kuti isachimwenso kwa chaka chimodzi kuti isalandile chilango chomwe bungweli linapeleka choti Wanderers isatenge nawo gawo pa mipikisano yonse m’dziko muno kamba konyanyala masewero a chikho cha Airtel Top 8.

 Pa 6 December chaka chatha, timu ya Wanderers inkayenera kusewera masewero ake achiwiri ndi timu ya Silver Strikers mu chikho cha Airtel Top 8, koma timuyi sinapite pa bwalo la masewero la Kamuzu munzinda wa Blantyre.

Timuyi inauza nyumba zofalitsa nkhani mdziko muno kuti iyo siyikanasewera masewero achiwiri ndi timu ya Silver pomwe inkafuna kukasuma pa chilango chomwe komiti yoyendetsa mipikisano ku bungwe la Football Association of Malawi linayipatsa kamba kosiyira masewero panjira mundime yoyamba ndi timu ya Silver ku Lilongwe.

Izi malingana ndi bungwe la FAM, kunali kulakwitsa kwambiri ndipo munchigamulo chomwe bungweli latulutsa Lachiwiri sabata ino chomwe chikalata chake wasainira ndi mlembi wa bungweli a Alfred Gunda, timuyi yomwe sizoni yapitayi yatuluka chi manjamanja, yapezeka yolakwa posapezeka ku masewero achiwiriwo.

Bungwe la FAM lagamura kuti timu ya ku Lali Lubani-yi isasewere nawoso mipikisano yose yomwe imayendetsedwa ndi bungweli komaso yalamulidwa kupeleka ndalama yokwana 1.5 miliyoni kwacha ngati chindapusa popezeka olakwa pa mlanduwu.

Koma ngakhale zili choncho, timu yovala makaka a “blue-yi”, yapulumukira mkamwa mwa mbuzi kamba koti FAM yachotsa chilango choti Wanderers isasewere nawo zikho ati kamba koti ndikoyamba kupalamura mlandu ngati umenewu koma siyikuyenera kupalamuraso mlandu ngati omwewu kwa chaka chimodzi kuyambira pa 1 January, 2024.

“Mighty Mukuru Wanderers idapezeka yolakwa kamba kolephera kupezeka pa Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre pamasewera a Airtel Top 8 quarter final ya 2023 zomwe ndikutsutsana ndi Article 10.6 ya malamulo oyendetsera mpikisano wa 2023 Airtel Top 8.

“Wanderers ikuyenera kupeleka chindapusa cha ndalama yokwana 1.5 miliyoni kwacha. Timuyi yaletsedwanso kuchita nawo mipikisano yonse yomwe imayendetsedwa ndi bungwe la FAM mu 2024, koma chilangochi sichigwira ntchito kwa miyezi 12 kuyambira pa 1 January 2024 pokhapokha ngati timuyi ingapezekenso yolakwa pa mlandu ngati womwewu,” yatelo mbali ina ya kalata ya FAM.

Bungwe la FAM lalalangiza timu ya Mighty Mukuru Wanderers za kufunika kolemekeza malamulo a masewero a mpira wa miyendo posatengera zomwe  zimachitika pamasewera, ndipo yanenetsa kuti malamulo a mpira akuyenera kutsatiridwa pofuna kulimbikitsa ndi kupeleka chikhulupiliro kwa okonda mpira wa miyendo komaso omwe amathandizira mipikisanoyi ndi ndalama.

Bungweli latiso lapanga chiganizo chokhululukachi ndicholinga chofuna kupititsa patsogolo masewero a mpira wa miyendo mdziko muno komaso yati vuto lalikulu lidachitika kamba kakulakwitsa kwa woyimbira masewero oyamba ndi Silver, a Godfrey Nkhakananga omwe anavomeleza kuti Silver Strikers yachinya chigoli cha chiwiri pomwe iwo omwe analiso ataimba kuti panali kukokanakokana.

Advertisement