Tisiyileni wathuyo pangani zanu – BBC yakwiyitsa anthu a ku Africa pa nkhani ya malemu TB Joshua

Advertisement
Prophet TB Joshua

Patadutsa zaka ziwiri ndi miyezi ingapo chimwalilireni mneneri TB Joshua ku Nigeria, wayilesi ya British Broadcasting Corporation (BBC) yabweletsa poyera zotsatira za kafukufuku yemwe inapanga pa zoipa zomwe a Joshua amapanga monga kugwililira amayi ndi atsikana ndi kuwakakamiza kuchotsa mimba komanso kupanga zozizwitsa zabodza.

Koma nkhaniyi yakwiyitsa anthu ochuluka m’mayiko a mu Africa omwe akuti BBC imadana ndi anthu a ku Africa ndipo ena ati BBC ikugwilitsidwa ntchito ndi satana.

Wayilesi ya BBC lero Lolemba pa 8 January, 2023 itulutsa gawo loyamba la kafukufuku yemwe ikuti yamuchita kwa zaka ziwiri pa momwe mneneri Temitope Balogun Joshua yemwe mwachidule amadziwika kuti TB Joshua amazunzira anthu aku mpingo wake wa Synagogue Church Of All Nations (SCOAN).

Mbali ina ya kafukufukuyu, wayilesi ya BBC yati yapeza kuti malemu TB Joshua omwe anamwalira pa 5 June chaka cha 2021, ankachitira nkhaza, kukhala pa maubwezi okakamiza ndi amayi amu mpingo wake ochokera maiko monga England, South Africa, Namibia ndi Nigeria.

Malingana ndi zomwe yalemba BBC pa tsamba lake la pa intaneti, Joshua anayamba kugwililira ambiri mwa amayiwa ali ndi zaka zosakwana 18 ndipo ena amawachita nkhazazi mpaka kwa zaka zisanu. Amayiwa awuza BBC kuti ena mwa iwo amawakakamiza kuchotsa mimba zomwe Joshua ankawapatsa.

Ena omwe ankagwira ntchito ndi Joshua awuza BBC kuti munthu wa Mulungu-yu ankapanga zozizwitsa zonama ponena kuti ankachita kugwirizana ndi anthu nseli.

BBC yati zotsatilazi, zomwe zitulutsidwe m’magawo atatu, zibweretsa mboni zosiyanasiyana omwe ambiri mwa iwo ndi ogwira ntchito akale, adindo akale komaso mamembala akale a mpingo wa SCOAN omwe malemu Joshua ankatsogolera omwe pano akutsogolera ndi mkazi wawo Evelyn.

Iyo yati anthuwa abweretsanso pa mbalambanda momwe malemuwa komaso akuluakulu ena mu mpingowu ankachitira zosaweruzika ndi azimayi komaso momwe mneneri Joshua ankachitila zozwizwitsa.

Nkhaniyi siyinisangalatse anthu ochuluka omwe ambiri mwa iwo ndi ochokera mmaiko amu Africa ndipo akudzudzula BBC kamba ka nkhani omwe ambiri akuti uku ndikungofuna kuyipitsa mbiri ya bwino yomwe malemu TB Joshua anasiya asanamwalire mu 2021.

Malingana ndi ena mwa mauthenga omwe tsamba lino lapeza pa masamba anchezo osiyanasiyana kuchokera Lamulungu pa 7 January, 2024 pomwe BBC inalengeza zoti itulutsa potsatira za kafukufukuzo, anthu ochuluka ati BBC yawonetseratu kuti imadana komaso simafuna kuyamikira anthu amayiko amu Africa.

“Inu anthu akumadzulo, lekani kuyang’anira pansi anthu amu Africa. Sitilinso ochepa mphamvu kuti tingakhale pansi pautsamunda wanu odzala ndi mabodza. Kudzikuza kwanu kunatiika pansi paukapolo.

“Malingaliro anu oyipa kwa Africa ndiomwe ayambitsa kafukufuku osavetsetsekayu. Ndi chifukwa chiyani koma?” wadabwa munthu wina pa fesibuku mu uthenga omwe anaulemba nchingerezi.

Munthu winaso yemwe anaikira ndemanga pa tsamba la fesibuku la BBC pomwe wayilesiyi inalengeza kuti iwulutsa za zotsatira za kafukufuku wakeyu, wauza wailesiyi kuti iyambe yapanga kafukufuku onga uyu pa anthu akhungu lachizungu.

“Pitani mukafufuze kaye za banja lachifumu. Mu Africa tili bwino kuno chonde TISIYENI,” wateloso kwina pa fesibuku pamene winaso wati: chonde kambani zambiri zokhudza mayiko 52 aku America.

Polembpo pa tsamba lake la mchezo, oyimba wa ku Malawi wa nyimbo za uzimu Shammah Vocals anati zomwe ikuchita BBC zikuoneka kuti ikugwilitsidwa ntchito ndi satana chifukwa Joshua anali munthu wabwino.

“Ndi zodabwitsa kuti anthu asankha kuona zoipa zomwe zalembedwa pa masamba a mchezo kusiya zabwino zomwe akuziona pa galaundi

“Anthu ambiri anamaliza maphunziro awo chifukwa cha Joshua, ena ali ndi nyumba kamba ka iyeyo ndipo ambiri anawapatsa chakudya iye ali moyo. BBC sinalembeko zimenezi koma lero yabwera ndikumati Joshua anali oipa. Iyi ndi ntchito ya satana mdyerekezi,” watero Shammah Vocals.

Advertisement