Ndine osalakwa, ndiloleni ndisankhe nawo Papa watsopano- walira mokweza Kadino Becciu

Advertisement
Cardinal Becciu

Ma Kadino akulu akulu a mpingo wa katolika, omwe anapatsidwa mphamvu zosankhanso mtsogoleri wa mpingowu, agwidwa kakasi kamba kakuti sanapange chiganizo ngati nkoyenera kuti Kadino yemwe anamangidwapo kamba ka utambwali ozembetsa ndalama aloledwe kulowa mchipinda chomata kuti asankhe nawo Papa kapena ayi.

Izitu zadza kamba ka Kadino Angel Becciu yemwe anali oyamba wa akulu akulu a mpingowu kumangidwa ndi Khothi la Vatican mchaka cha 2023 kamba kowononga ndalama komanso kuchita chinyengo ndipo adalamulidwa kuti akaseweze jele kwa zaka zoposa Zisanu.

Mkuluyu, asadamangidwe, anachotsedwa pa undindo osankha munthu yemwe ali oyera mchaka cha 2020 ndi Papa Francis yemwe pa nthawiyo adamuwuziratu kuti wataya naye chikhulupiliro ndipo sakumufunanso pomwe anamuwuza kuti ndi wa tsankho komanso wakuba.

Koma a Becciu, omwe akhala akukana milanduyi pa nthawi yomwe adapanga apilu, ati panopa ndi oyera ndipo akuyenera kuloledwa kuti alowe mchipinda chomatachi ndikusankha nawo Papa watsopano.

Iye wati adakumana ndi Papa Francis m’mwezi wa January pomwe adamuwuza kuti “ndapeza mayankho pa nkhani yanu” koma mkumano wina sunatheke kamba kakuti Papayu adagonekedwa m’chipatala mwezi wa February.

Ndipo a Becciu ati sakudzuwa ngati malemu Francis adasiya kalata iliyonse yokhudza nkhani yawo.

Ngakhale izi zili motere, likulu la mpingowu kudzera mwa m’neneri wake Matteo Bruni, akukanitsitsa mwa mtu wa galu kulankhurapo pa za nkhaniyi pomwe ma Kadino odutsa zaka 80 omwe ndi 135 ali ovomerezeka kuponya voti yosankha mtsogoleri watsopano wa mpingowu.

Pakadali pano, a Becciu ali m’gulu limodzi la ma Kadino omwe sakuloledwa kuponya nawo voti, zimene sizidasangalatse mkuluyi yemwe wanenetsa kuti ngosalakwa ndipo akuyenera aponye nawo voti.

Ma Kadino a mpingowu akumana kuyambira pa 6 May mwezi wa mawa kuti ayambe zofuna kusankha Papa watsopano.

Papa Francis ayikidwa m’manda Loweruka pomwe adamwalira Lolemba lathari patangodutsa maola ochepa chabe iyeyu atapereka mafuno abwino a chikondwelero cha ku ukanso kwa Ambuye Yesu.

Papa yemwe asankhidwe, adzakhala mtsogoleri wa akhristu a mpingowu omwe ndi oposa 1.3 billion pa dziko lonse.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.