Pasuwa wayitana anyamata kukonzekera CHAN

Advertisement
Flames

…Ekhaya yasonkha nawo…

Timu ya Ekhaya yomwe yangolowa kumene mu mpikisano wawukulu m’dziko muno yasonkha nawo osewela pa mndandanda wa anyamata 25 omwe mphunzitsi wa timu ya mpira wamiyendo ya Malawi Kalisto Pasuwa wayitana, kukakonzekere kuswana ndi South Africa.

Malawi ikumana ndi South Africa m’masewelo oyamba a mu mpikisano wa African Nations Championship qualifiers pa 03 May pa bwalo la Bingu, ndipo nkhondo yachibweleza idzafumbira sabata yotsatila yakeyo pa 11 May 2025 pa bwalo la Loftus Versfeld m’dziko la South Africa.

Anyamata asanu ndi atatu achoka ku FCB Nyasa Big Bullets, asanu (5) kuchoka ku Mighty Wanderers, asanu ndi m’modzi (6) kuchoka ku Silver Strikers, awiri achoka ku Kamuzu Barracks, ndipo Ekhaya, Mighty Tigers, Moyale ndi Dedza Dynamos asonkha m’modzi-m’modzi kuti akakonzekere kuzigulira malo mu mpikisano wa CHAN omwe umayitana osewera ake ndi a ma timu a m’dziko momwemo okhaokha basi.

Masewelo onse omwe Malawi yasewela chaka chino yapambana ndi Comoros kawiri ndi kugonjanso ndi Tunisia ndi Namibia pomwe Bafana Bafana yapambana masewelo ake onse kufananitsa mphamvu amodzi ndi Egypt.

Mndandanda onse uli motere ;

Goalkeepers

1. Richard Chimbamba

2. George Chikooka

3. Lucky Tizola

Defenders

1. McDonald Lameck

2. Nixon Mwase

3. Maxwell Paipi

4. Khumbo Banda

5. Fanizo Mwansambo

6. Emmanuel Nyirenda

7. Andrew Jovinala

8. Alick Lungu

Midfielders

1. Yankho Singo

2. Lloyd Aaron

3. Chawanangwa Gumbo

4. Wongani Lungu

5. Charles Nkhoma

6. Zebron Kalima

7. Blessings Singini

Strikers

1. Zeliat Nkhoma

2. Elson Kanjira

3. Binwell Katinji

4. Wisdom Mpinganjira

5. Gaddie Chirwa

6. Promise Kamwendo.

7. Chikumbutso Salima

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.