Yalimba nkandilo! Pomwe a Kondwani Nankhumwa, a Grezelder Jeffrey komanso a Cecilia Chazama amafuna bwalo la apilo liwabwezeretse pa maudindo awo mu chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive (DPP) komaso kuwapatsa chiletso kuti asakaonekere ku komiti yosungitsa mwambo mchipani, bwaloli lakana mapemphowa ndipo atatuwa akuyeneraso kupeleka ndalama zomwe zagwiritsidwa ntchito pakumva mlanduwu.
Atatuwa anakamang’ala ku bwalo la apilo kamba koti sanakhutitsidwe ndi chigamulo chomwe bwalo la milandu ku Lilongwe linapeleka pomwe atatuwa anakadandaula za kusinthidwa maudindo awo ndi mtsogoleri wa chipani cha DPP a Peter Mutharika kumapeto kwa chaka chomwe changothachi, 2023.
Bwalo la milandu ku Lilongwe-ko linagamula kuti panalibe vuto lili lonse kuti atatuwa asinthidwe maudindo awo ponena kuti atatuwa analephera kupititsa kubwaloko umboni oti anaaaphwanyilidwa ufulu pa ndale kamba ka kusinthidwa maudindo kwawo ndipo analamulidwaso kuti alipile ndalama zomwe zinagwiritsidwa ntchito pa mlanduwo.
Izi sizinasangalatse atatuwa omwe anapitaso ku bwalo la apilo munzinda wa Blantyre pomwe anatsindika kuti malamulo achipani amati maudindo awowo atha kusinthidwa kudzera ku koveshoni kokha osati zomwe mtsogoleri wa chipanichi a Mutharika anapanga ndipo anapemphaso chiletso kuti iwo asakaonekere ku komiti ya chipani yosungitsa mwambo.
Koma oweluza milandu ku bwaloli a Justice Dorothy Nya Kaunda akana mapempho onse omwe anthuwa anapititsa ku bwaloli ndiposo walamura kuti atatuwa alipileso ndalama zomwe zagwilitsidwa ntchito pa mlanduwu.
Chipani cha DPP kudzera mwa a Mutharika, chinachotsa a Nankhumwa pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi mchigawo chakumwera, mmalo mwawo munalowa a George Chaponda ndipo iwo anasankhidwa kukhala mlangizi wawa a Mutharika pamodzi ndi a Chazama omwe anali mkulu wa amayi mchipanichi ndipo mmalo mwawo munalowa a Mary Thom Navicha.
Kupatula apo, mayi Jeffrey omwe anali mlembi wamkulu wachipanichi anawasankha kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani mchigawo chapakati ndipo m’malo mwawo munalowa a Clement Mwale zomwe zinakwiyitsa makosanawa ndipo anapempha khothi kuti iwo abwezeretsedwe m’maudindo awo.