Mukaona amuna kapena akazi ochita maukwati okhaokha gendani, watero pulezidenti wa ku Burundi

Advertisement
Burundi president Evariste Ndayishimiye

Mtsogoleri wadziko la Burundi Evariste Ndayishimiye yemwenso ndi mkatolika, wadzudzula mayiko a azungu kamba kolimbikitsa ma ufulu oti amuna kapena akazi azikwatirana okhaokha.

Mkunena kwake wati izi ndizonyasa komanso zamalawulo kotero oterewa akapezeka aziyikidwa mbwalo la masewero ndikuponyedwa miyala.

Iye wadzudzula mayiko a azungu omwe amalimbikitsa mayiko ang’onoang’ono kuti alole maukwati a amuna kapena akazi okhaokha ndicholinga choti azilandila thandizo, ponena pake wati “Asiyeni asunge chithandizo chawo.”

“Ineyo pandekha, ndikuganiza kuti tikaona anthu ngati amenewa ku Burundi, tiziwayika m’bwalo lamasewera n’kuwaponya miyala. Ndipo sikungakhale tchimo kwa amene atero,” adatero.

Ndayishimiye pa mwambo wina omwe unachitika mdzikolo zomwe zidaulutsidwa ndi atolankhani amdzikoli.

Mtsogoleriyu anati anthu omwe ndi amdzikoli koma akukhala kunja kwa dzikolo ngati asankha mdyerekezi ndikuchita zogonana amuna kapena akazi okhaokha sayenera kubwerera mdzikolo.

M’mbuyomu dziko la Uganda lidachotsa lamulo lovomereza amuna kapena akazi kukwatirana okhaokha, zomwe zidayambitsa mkwiyo pakati pa mabungwe omenyera ufulu ndi mayiko akwa Zungu.

Poyankhapo, Washington idati ichotsa dziko la Uganda ku mgwirizano waukulu wamalonda ndipo yakhazikitsa ziletso za visa kwa akuluakulu ena, pomwe Banki Yadziko Lonse idayimitsa ngongole zatsopano mdzikolo.

Advertisement