Anthu a ku Malawi ayamba kupha makwacha pa YouTube ndi Fesibuku mu 2024


A Malawi konzekani. Tsopano kukhala kupha makwacha kudzera pa tsamba la mchezo la Fesibuku komanso pa YouTube kuyambira chaka chomwe tichiyambe mawali cha 2024.

Izi zili chomwechi malingana ndi zomwe wanena mkulu wa bungwe la MACRA a Daudi Suleiman.

Iye wati tsopano dziko la Malawi lilandira chilolezo choti anthu azitha kupeza ndalama kudzera pa masambawa.

Mkunena kwawo, a Suleiman ati iyi ndi nkhani yabwino ku mtundu wa aMalawi  ponena kuti zithandiza anzathu omwe amapanga zinthu zoti awonere kuti azipeza phindu.

Dziko la Malawi ndi dziko limodzi lomwe linalibe chilolezo choti anthu azitha kupeza phindu kudzera pa masamba a mchezowa.

A luso ambiri monga oimba ndi ochita zisudzo a ku Malawi  kuno amaika zinthu zawo pa YouTube ndi pa Fesibuku ndipo akhala ndi mwayi opindula nawo chaka mawachi.