Alimi samalani: Bambo amunjata kamba kogulitsa feteleza wachinyengo

Advertisement

Apolisi ku Kasungu amanga a James Phiri a zaka 36 zakubadwa kamba kopezeka akugulitsa zinthu zonga ngati feteleza zomwe anazipakira m’matumba a feteleza ndikumagulitsa ngati feteleza.

Mkuluyu wamangidwa dzulo kutsatira anthu ena omwe anatsina khutu a polisi pa zankhaniyi ndipo anachita kafukufuku mtauni ya Kasungu ku shopu ya mkuluyu ndipo anapezadi feteleza wachinyengoyu atapakilidwa m’matumba a NPK wa kampani ya Superfert.

Apa apolisiwo analanda matumba okwana 18 afeteleza wachinyengoyu kuti akamuyese ngati ndi feteleza weni weni. Kenako anamuthira unyolo mkuluyu.

Izi zikuchitika pomwe nyengo ino ndi yadzinja ndipo alimi osiyanasiyana amakhala kalikiliki kugula feteleza oti akathire m’minda yawo ndicholinga choti awonjezere chonde mthaka.

Mkuluyu amutsekulira mlandu opezeka ndi feteleza wachinyengo ndipo pompano akaonekera ku bwalo la milandu kukayankha pazokhudza mlanduwu.

A Phiri amachokera m’mudzi wa Mbeta kwa mfumu yayikulu Kholoni m’boma la Lilongwe.

Advertisement