Black Nina anatenga njinga yake kuti ‘akweze mundege’

Advertisement
Black Nina at an airport in Malawi where he wanted to carry his bicycle into a plane

Black Nina yemwe ndi oyimba odziwika bwino m’dziko lino, anapita ku malo okwerera ndege ndi mpanda buleki (njinga)  wake uku atanyamulirapo chibinyira cha zovala ndicholinga choti akweze njingayo mundege pawulendo wake waku jubeki.

Malingana ndi kanema yemwe anthu ena anajambula pozizwa ndi zomwe woyimbayu anapanga, zimaonetsa kuti alonda pamalopo anamubweza nayo njingayi kuti asafike nayo pamalopo.

Pa tsamba lake la mchezo, Black Nina wadandaula kuti “Andilakwira”

Koma anthu ena pa masamba a mchezo ati akuona kuti oyimbayu anangochita izi ngati njira imodzi yochititra zisudzo.

Aka sikoyamba mkuluyu kuyenda pa njinga akakhala kuti akukayimba ndipo ena akuti ndi chizolowezi chake.

Oyimbayu lero wapita mdziko la South Africa komwe akuyembekezereka kukayimba m’malo osiyanasiyana munyengo ino ya khisimisi.

Advertisement