Kuno ayi – ansembe Akatolika aletsedwa kudalitsa maukwati a amuna kapena akazi okhaokha

Advertisement
Pope Francis has approved the blessing of same-sex marriage in Catholic Church

Ma bishopu a mpingo wa Katolika pansi pa bungwe lawo la Episcopal Conference of Malawi (ECM), ati zomwe wanena mtsogoleri wa mpingowu papa Francis sizikutanthauza kuti mpingowu waloleza maukwati a amuna kapena akazi okhaokha ndipo anenetsa kuti palibe wansembe amene aloledwe kudalitsa maukwati oterewa kuno ku Malawi.

Izi zikudza kutsatira nkhani yomwe yadziwika lachiwiri pa 19 December yomwe imafotokoza kuti mtsogoleri wa mpingowu a Papa Francis alamula kuti maukwati a anthu ofanana ziwalo atha kumadalitsidwa tsopano mumpingowu.

Koma bungwe la ECM kudzera mu chikalata chomwe latulutsa, lati zikuoneka kuti pali kusavetsetsa pa nkhaniyi zomwe akuti zikubweretsa mafuso a nkhaninkhani, nkhawa komaso manong’onong’o makamaka pakati pa anthu omwe amakonda ndi kutsatira ziphuzitso za mpingowu.

Mukalatayi yomwe yasayinidwa ndi atsogoleri ake onse asanu ndi anayi (9) omwe ndi kuphatikizapo mtsogoleri wa mkulu, Archbishop George Desmond Tambala, bungwe la ECM lati kalata yomwe wavomereza Papa Francis, sikuti ikuvomereza kudalitsa maukwati a anthu ofanana ziwalo ngati momwe ena akuganizira.

Bungweli lati zomwe wanena Papa Francis zimatanthauza kuti maukwati ovomerezeka ndi a pakati pa mwamuna ndi mkazi ndipo kuti kudalitsidwa komwe kukunenedwa ndikokhudza chinthu chili chonse chomwe chikufuna mdalitso wa Mulungu osati maukwati a amuna kapena akazi okhaokha.

“Bungwe la Episcopal Conference of Malawi likufuna kufotokozera momveka bwino pa nkhani yokhudza kulengezedwa kwa nkhani yokhudza mdalitso (Fiducia Supplicans). Ife, ma Episkopi anu, taona kutanthauzira kolakwika kwa chilengezochi komwe kwadzetsa chidwi, mantha ndi nkhawa pakati pa Akatolika ndi anthu omwe amayang’ana ku tchalitchi cha Katolika kaamba ka chitsogozo cha makhalidwe, uzimu ndi chiphunzitso.

“Kulengeza sikukukhudza dalitso la maukwati a amuna kapena akazi okhaokha komanso kuvomereza kwa sakramenti zofanana ndi maanja. Ayi.” yatelo mbali ina ya kalatayi.

Powopa kubweretsa chisokonezo mu mpingo wa Katolika m’dziko muno, bungwe la ECM lalamura kuti maukwati antundu uli onse okhudza amuna kapena akazi okhaokha ndiosaloledwa.

“Pofuna kupewa kubweretsa chisokonezo pakati pa okhulupilira, tikulamula kuti pazifukwa zaubusa, madalitso amtundu uliwonse okhudza maukwati a amuna kapena akazi okhaokha amtundu uliwonse, siwololedwa m’Malawi.

“Tikufuna titsimikizile Akatolika onse ndi onse amene ali ndi chidwi ndi chiphunzitso cha Katolika kuti chiphunzitso cha ‘One Holy Catholic and Apostolic Church on Marriage’ chikadali chimene chasonyezedwa m’Ndime 4: ‘mgwirizano wapadera, wokhazikika, ndi wosathetsedwa pakati pa mwamuna ndi mkazi, umatsegura m’badwo wa ana’,” Yatelo mbali ina ya kalatayi.

Advertisement