Afisi avuta kwambiri ku Machinga

Advertisement

Anthu akudera la mfumu yaikulu Mtumbwinda m’boma la Machinga, akukhala mwa mantha kamba ka afisi olusa omwe akuti kumayambiliro a mwezi uno apha munthu m’modzi komaso loweluka lapitali avulazaso munthu wina.

Yatsimikiza za nkhaniyi ndi mfumu yaikulu Mtumbwinda yomwe inabadwa Franklin Chikwewu Chome yomwe yati nyama zolusazi zinayamba kalekale kuvutitsa kudera lakeli.

Mfumu ya ndodoyi yati usiku wa pa 6 December chaka chino, Austin Kachingwe yemwe anali msodzi ndipo amachokera m’mudzi mwa mfumu Vethiwa m’boma lomweli, ankachokera ku nyanja ya Chiuta komwe anapita kukatchera miyono yake kuti aphe nsomba.

Mfumu Mtumbwinda yatiuza kuti Kachingwe, yemwe anali osapitilira zaka 35, pomwe amabwelera kupita m’mudzi mwa Nyenga momwe anakwatira, anakumana ndi afisiwa pa madambo omwe ali pakati pa mudziwu ndi nyanja ya Chiuta ndipo nyama zolusazi zinayamba kumukhadzulirana mosamva chisoni.

Atamva kulira kwa munthuyu komaso phokoso lomwe afisiwa amapanga pa nthawiyi, anthu omwe nyumba zawo zili pafupi ndi malo omwe panachitikira ngoziyi, anathamanga kuti akamupulumutse Kachingwe koma momwe amafika afisiwa omwe akuti anali osachepera asanu ndi anayi (9), anali atamuvulaza kwambiri munthuyo.

“Patsikuli Austin Kachingwe atamaliza kutchera miyono yake pa nyanja ya Chiuta, anayima kaye kwa nzake wina ndikumacheza. Ndiye cha ma 8 koloko usiku anayamba ulendo opita kwawo, m’mudzi mwa Nyenga komwe anakwatira ndipo anakumana ndi afisiwa pa dambo lina pomwe anthu amalimapo mpunga.

“Anthu atamva kukuwa kwa malemuwa komaso phokoso la afisi, adathamangira kuti akawone chomwe chikuchitika ndipo ndi pomwe anawona afisi aja akuthawa koma anali atamuvulaza kale kwambiri munthu uja. Anali atamung’amba pa mimba, matumbo ali pantunda komaso ziwalo zina zitadyedwa kale. Anthu aja anamupeza munthuyu asanatsilizike koma atatheratu moti kuyankhula kwake komaliza anangoti ndataya foni, kenaka anatsilizika, kutisiya,” yatelo mfumu yaikulu Mtumbwinda.

Iwo ati nkhaniyi inakasiyidwa ku polisi ya Chikwewu omwe anapita pa malo angoziwa m’mawa wa pa 7 December, 2023 tsikuso lomwe thupi la malemu Kachingwe linalowa m’manda ku mudzi kwawo kwa Vethiwa.

Mfumuyi yati khonsolo ya bomali inatumiza mlenje kuti akathane ndi nyama zolusazi koma akuti zimapezeka kuti pomwe mlenjeyu ali ku phiri kusaka dzilombodzi, afisiwa amakhala ali m’mamidzi ndipo mlenjeyu akafika ku mamidziko, afisiwa amakhala akuveka kulira ku mapiri ndipo izi akuti zachitika kangapo kufikira pomwe mlenjeyu anaitanidwa kukagwira ntchito yonga yomweyo m’boma la Mangochi.

Mfumu Mtumbwinda yatsimikizaso kuti loweluka lapitali pa 16 December, 2023 afisiwa avulazaso munthu wina wotchedwa Bakayawo wa m’mudziso mwa Nyenga yemwe amachokeraso kokapha nsomba ku nyanja ya Chiwuta ndipo mfumuyi yapempha nthambi yoyang’anira zanyama komaso akuluakulu ena kuti achitepo kanthu ponena kuti nyamazi zikupeleka chiopsezo chachikulu ku anthu amdelari.

“Loweruka lapitali pa 16 December munthu winaso yemwe timati Bakayawo anakumanaso ndi afisiwa akuchokera ku nyanja. Koma mwa mwayi, iyeyu sanatisiye, koma amuvulaza kwambiri m’mutu, manja ndi miyendo. Kudera kuno anthu ali pa chiopsezo kwambiri. Tipemphe akuluakulu athu koti chonde atithandize nsanga,” yapempha mfumu yaikuli Mtumbwinda.

Iwo ati afisiwa akupeleka chiopsezo kwa anthu amidzi yochuluka kudera lawoli kuphatikizapo asodzi omwe akuti amayenda usiku kupita ku nyanja ya Chiuta kukapha nsomba kuti apeze thandizo la m’makomo awo ndipo ati ngakhale nyamazi zili zotetezedwa, sizikuyenera kupeleka chiopsezo kwa anthu.

Advertisement