SRWB yati anthu ena amene analumikizilidwa madzi mwaulele sakulipira ma bilu

Advertisement
Rita Makwangwala SRWB spokesperso

Bungwe lomwe limawona za madzi mchigawo chakum’mwera la Southern Region Water Board (SRWB) lati anthu ena omwe akumalumikizilidwa madzi mwaulele sakulipira ma bilu a madzi chifukwa akumayesa kuti madziwo adzimwanso ulele

Wofalitsa nkhani ku Bungwe la SRWB Rita Makwangwala ndiyemwe wayankhula izi ku Salima pansonkhano wapa chaka wa atolankhani a Bungwe la Zomba Press Club.

Makwangwala wati anthu ambiri omwe adalumikidzilidwa madzi mwaule sakumalipira madzi popeza akuganidzanso kuti madziwo ndi awulele.

Pamenepa iye wapempha atolankhani kuti azilemba nkhani zodziwitsa anthu omwe adalumikidzilidwa madzi mwaulele komanso anthu ena onse za ubwino wolipira ma bill amadzi ku Bungwe la SRWB.

Makwangala adayamikira bungwe la atolankhani a Zomba Press Club chifukwa cha ubale wabwino omwe ulipo ndi bungwe la SRWB chifukwa pazochitika zambiri monga kudzala mitengo pa Phiri la Zomba amakhalira limodzi chaka chilichonse.

“Ife a Bungwe la SRWB tipitiliza kukwaniritsa cholinga cha Boma popereka madzi awukhondo kwa anthu mchigawo chaku mwera.” Adatero Rita Makwangwala.

Wofalitsa nkhani ku Bungwe la SWRB yu adapemphanso atolankhaniwa kuti adzilembanso nkhani zochonjedza anthu zokuyipa kolumikiza madzi munjira yokuba komanso kuwononga zipangizo zomwe amagwiritsira ntchito popereka madzi kwa anthu.

Makwangala wati Bungwe la SRWB likumakumana ndi mavuto opereka madzi kwa anthu chifukwa anthu ena akumaba zipangizo za bungweli monga ma payipi komanso iye adati pali anthu ena akumalumikidza madzi okha munjira yokuba.

Advertisement