Khonsolo ya Balaka itsutsa zoti yatseka sukulu chifukwa cha njala

Advertisement

Khonsolo ya Balaka yatsutsa mphekesera zomwe zakhala zikuzungulira m’masamba a mchezo osiyanasiyana apa makina a intaneti onena kuti boma latseka sukulu ya pulaimale ya Naliswe yomwe ili m’bomali kamba ka njala yomwe akuti yafika posauzana mdelari.

Malingana ndi mneneri wa khonsolo ya Balaka, Mary Makhiringa, maphunziro pa sukuluyi akupitilira monga mwa nthawi zonse ndipo zomwe zakhala zikukambidwazi ndi bodza lamkunkhuniza.

”Ife monga khonsolo tidali odabwa ndi zomwe zakhala zikuzungulira m’masamba a mchezo osiyanasiyana kunena kuti boma latseka sukulu ya Naliswe chifukwa cha njala. Ndi zoona inde kunena kuti njala yakhudza madera ambiri mdziko muno kuphatikizanso boma la Balaka. Komabe, ife ngati khonsolo tilibe mphamvu zotseka sukulu kamba ka njala,” adafotokoza Makhiringa.

A Makhiringa adawonjezeranso kunena kuti akuluakulu a  khonsolo ya Balaka adakayendera sukuluyi ndipo adapeza maphunziro ali mchimake monga mwa nthawi zonse.

Iwo adawonjezeranso kunena kuti zithunzi zomwe zikuzungulira mu masamba a mchezo zikuwonetsa ana atavala yunifolomu ya makaka a buluu  pomwe yunifolomu ya sukulu ya Naliswe ndi ya makaka obiliwira.

Advertisement