Yudasi! Mchimwene wavomera kuti anatenga gawo pa imfa ya Agnes Katengeza

Advertisement

Odya naye mbale imodzi ndiye okupelekayo; ndipo monga m’mene Yudasi anapelekera Yesu kuti aphedwe, mchimwene wa malemu Agnes Katengeza wavomera kuti anatenga gawo lalikulu pa imfa ya m’bale wakeyo yemwe amakhala naye nyumba imodzi.

Mneneri wa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu atsimikiza zakumangidwa kwa Amos Katengeza wa zaka 27, yemwe akuti ndi mchimwene wa Agnes ndipo akuti awiriwa amakhalira limodzi mu mzinda wa Lilongwe.

Kupatula apo, lipoti la apolisi likusonyeza kuti kugwidwa kwa Amos ndi kamba koti apolisi akhala akusakasaka ma foni komaso katundu osiyanasiyana yemwe anabedwa kumayambiliro kwa September malemu Agnes yemwe anali ogwira ntchito ku Reserve Bank, asanaphedwe.

Pomwe apolisiwa amafufuza za iPhone 6 yomwe inabedwayo, foniyo inapezeka ndi munthu wina okoza mafoni ku Blantyre ndipo munthuyo adavomera kuti adalandira iPhone 6 komaso iPhone 13 kuchokera kwa Amos Katengeza yemwe akuti amafuna amuchotsere manambala a chinsinsi.

Apa ndi pomwe anayamba kusakasaka Amos ndipo lipoti la apolisilo lasonyeza kuti mkuluyu wavomera kuti anatengadi gawo pa kuphedwa kwa mchemwali wake Agnes amene thupi lake linapezeka kumbuyo kwa galimoto ya ku ntchito yomwe amayendera.

“Atafufuza chikwama chake (Amos), adapezeka ndi iPad ndi power bank, yemwe ndi katundu wa malemuyo (Agnes) yemwe adabedwa panthawi yakuphedwa kwake. Wokayikilidwayo amabisa komwe adagulitsa laputopuyo koma apolisiwo adakwanitsa kupeza laputopu ya ENVY HP kwa wabizinesi wina mkati mwa nsika wa Blantyre yemwe adavomera kuti adalandira katunduyo kuchokera kwa woganiziridwayo.

“Amos wavomereza mosakakamizidwa kuti anachitapo kanthu pa kupha mwankhanza kwa malemuyo (Agnes). Logi ya foni yake inasonyeza kuti anali pamalo pomwe anatayira mtembo wa malemuyo,” likutero lipoti la apolisi lomwenso lati izi zatsimikiziridwa ndi kanema wa CCTV.

Malinga ndi Apolisi, Agnes atangophedwa kumene, anzake a Amos adasiya zinthu zonse m’manja mwake monga gawo la malipiro ake kuphatikizapo ndalama zomwe adamulonjeza kuti amupatsa ndipo kenaka Amos adatumiza zinthuzo kwa bwenzi lake ku Blantyre kudzera njira yotumizila katundu (courier services).

Pakadali pano apolisi akusaka anthu ena omwe akuwaganizila kuti adatengapo gawo pa imfayi.