Kwakwana-kwakwana tiyeni tipatsane ulemu – Chisale

Advertisement
Chisale

Mkulu wa achinyamata mu chipani cha Democratic Progressive (DPP) a Norman Chisale achenjeza anthu ena omwe akulondalonda iwo komanso otsatira chipani cha DPP kuti tsiku lina adzabwezera, ndipo apolisi omwe adawombera m’modzi wa ma membala awo amudziwa ndipo adzamumanga pa 17 September.

Poyankhula pamene amapelekeza a Alfred Gangata lero ku Lilongwe pomwe amatuluka mu chitolokosi cha apolisi kudzera ku bwalo la milandu, a Chisale omwe ndi wachitetezo wa mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika ati pali anthu ena omwe amafuna kuwapanga chipongwe pa Shoprite ndipo ati tsiku lina adzabweza.

Iwo atinso onse ofuna kuwamanga azibwera ndi zikalata zochoka Ku bwalo la milandu zowamangira(warrant of arrest), pamene ati asamangobwera ndi mapazi opotoka.

A Chisale ati kuwombeledwa kwa m’modzi mwa owatsatira awo kudachitika chifukwa iwo padalibe.

Otsatira chipani cha DPP kudzera mwa mkulu owoyang’anira amayi a Mary Navicha anadandaula mchitidwe omwe apanga apolisi ponena kuti apolisi ndiwo awombela a Brenda Saidi pa mkono.

Koma malinga ndi newspaper ya nation ya pa 13 achipatala ati bala la a Saidi si bala la chipolopolo ndipo apolisi akana kuti sanawombere aliyense otsatira chipani cha DPP.

A Alfred Gangata anapita ku chipatala kukawona a Brenda Saidi pomwe amachokera ku bwalo la milandu kutsatira kuwamanga kwawo lachisanu pa mlandu osema zikalata zabodza za bungwe lotolera misonkho la MRA mzaka za 2017 ndi 2018, ndipo ati apeleka ndalama zonse zomwe achipatala awatchaje a Saidi chifukwa chokhala mchipatala.