
Wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha Democratic Progressive (DPP) mchigawo cha pakati, a Alfred Gangata ati tsopano boma layamba kumanga anthu m’malo mothana ndi mavuto omwe dziko likukuna nawo pakadali pano.
Polankhula pomwe amapita kunyumba kwawo kuchokera ku bwalo la milandu, a Gangata ati pakali pano boma likuwamanga ndi cholinga choti asapangitse misonkhano ndipo ati pamenepa ndi pomwe awatokosola kuti achititse misonkhano yambiri.
A Gangata apempha anthu otsatira chipani cha DPP kuti adekhe pamene nkhani yawo ili ku bwalo la milandu ndipo ati salankhulapo zambirii pa izo ponena kuti nkhani ili kubwalo ndipo alole bwalo la milandu lipeze kuti Iwo ndi olakwa kapena osalakwa.
A Gangata adawamanga lachisanu mu mzinda wa Lilongwe pa chifukwa chosema zikalata zabodza za bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA).
A Gangata ndi m’modzi mwa otsatira chipani cha DPP omwe amangidwa pambali pa kumangidwanso kwa a Joseph Mwanamveka, a Sameer Suleman mwa ena pa milandu yosiyana siyana.