
Walonjezanso ntchito za nkhani nkhani, 100 biliyoni kwa boma lilironse
Yakwananso nthawi ya malonjezo. Mtsogoleri wa chipani cha UTM a Dalitso Kabambe wati iwo akalowa m’boma pa Sepitemba pano, mitengo ya Feteleza itsika. Kusiyana ndi kale pamene chipanichi chinati anthu azizagula pa mtengo wa MK4500, ati tsopano afika pa mtengo wa MK45000.
Polankhula pa msonkhano wa atolankhani omwe adachititsa ku likulu la chipanichi, a Kabambe ati a Malawi akonzekere kuyimba lokoma chipani cha UTM chikalowa m’boma mu Sepitemba muno.
“Pa nkhani ya Feteleza, tawelengera kale masamu ake ndipo taona kuti mtengo wake suzadutsa MK45000,” anatelo a Kabambe akutsindika kuti iwo ndi amene adakhazikitsa nawo ndondomeko ya Starter Pack ya boma la a Muluzi.
Atafunsidwa kuti a Malawi awakhulupilire bwanji pamene mmbuyomu chipanichi chidalonjeza mtengo wa MK4500, a Kabambe anati chipani chawo sichidangolonjeza mtengowu koma chinakwaniritsa.
“Chaka choyamba cha Tonse Feteleza adali pa MK4500, inali UTM imene ija,” iwo anatelo kuonjezera kuti zinthu zinasintha ati pomwe a Chakwera adayamba kusala anthu a UTM mu boma.
A Kabambe anawonjezera kunena kuti akalowa m’boma, ati boma lilironse mu dziko muno azizalipatsa MK100 billion pa chaka ya chitukuko. Izi ati zidzakhala ngati m’mene amachitira mayiko a Amereka ndi United Kingdom.
“Ndikufuna maboma azizachita mpikisano pa chitukuko, ndiye ndizizawapatsa ndalama zimenezi,” anatero a Kabambe uku otsatira chipani akuomba m’manja.
Iwo adafotokozanso kuti cholinga chawo ndi kukonza ulimi ndi kuzasintha chuma kuti ntchito ziyambe kupezeka kwa a Malawi.
“Tizatsegula fakitale, tizalimbikitsa ulimi komanso ntchito zokopa alendo. Tikatero ntchito zizapezeka zochuluka,” iwo anatero.
Msonkhano wa atolankhani uwu umachitika pomwe dziko lino likudutsa mu nyengo zowawa. A Kabambe anadzudzula utsogoleri wa a Chakwera ati kamba kowalephera a Malawi.