Mnyamata wa zaka 16 wagwililira gogo wa Zaka 74

Advertisement

Apolisi m’boma la Ntchisi akusunga mchitokosi mnyamata wa zaka 16 atagwililira  gogo wa zaka 74.

Malingana ndi Mneneli wa apolisi  ku chigawo cha pakati kum’mawa a Esther Mkwanda, nthawi ya kumasana pa tsikuli  mnyamata anatsatila  kumunda komwe gogoyu amakasaka nkhuni ndipo anamumanga manja ndi kukolopola zovala za gogoyu mkumuchita za kusalungamazo.

Apolisi ati gogoyu anakafotokozera nkhaniyi kwa mwana wawo wamkazi yemwe anatengela nkhaniyi ku polisi  m’bomali, ndipo zotsatilanso za chipatala zinatsimikiza za kugwililidwaku.

Apolisi ati mnyamatayu ali mmanja mwawo kuyembekezera kukayankha mulandu ogwililira.

Advertisement