Mutharika wachotsa Nankhumwa pa udindo

Advertisement
Malawi President Peter Mutharika and Kondwani Nankhumwa

Kuli kanthu kokanthula nchala mchipani cha Democratic Progressive (DPP) pomwe mtsogoleri wake a Peter Mutharika achotsa a Kondwani Nankhumwa pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi mchigawo chakum’mwera.

Izi ndimalinga ndi kalata yomwe chipani cha DPP yatulutsa lamulungu pa 10 December, 20 yomwe wasainira ndi mtsogoleri wa chipanichi a Mutharika.

Malingana ndi chikalatachi, a Mutharika asankha a George Chaponda kulowa mmalo mwa Nankhumwa pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi mchigawo chakummwera.

Chikalatachi chikusonyezaso kuti a Nankhumwa komanso Cecilia Chazama yemwe anali mkulu wa amayi mchipanichi awasankha kukhala alangizi a Mutharika.

Kupatula apo, a Mary Navicha awasankha kulowa m’malo mwa Chazama ngati mkulu wa amayi watsopano mchipanicha DPP.

Zonsezi zikuchitika pomwe mchipanichi muli kusamwerana madzi makamaka pa nkhani ya maudindo osiyanasiyana.

Pakadali pano a Nankhumwa sanayankhule pakusinthidwa kwawo udindowo ndipo anthu a kuti izizitha kupangitsa kuti kusagwirizana komwe kulipo kufikile mlingo wina tsopano.

Advertisement