Maanja oposa 5,000 akusamutsidwa m’madera a ngozi ku Nsanje

Advertisement

Nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzi m’dziko muno ya DoDMA yati ili nkati mosamutsa maanja oposa 5,000 ku dera la Makhanga m’boma la Nsanje, omwe amakhala m’malo a ngozi za madzi osefukila.

Malingana ndi nthambiyi, ntchitoyi ikuchitika mogwirizana ndi khonsolo ya boma la Nsanje ndipo maanja oposa 3,500 asamuka kale pakadali pano akukhala mmalo otetezeka.

Nthambiyi yati ntchito yosamutsa anthuwa yakhala yovuta chifukwa magalimoto sakufika m’mdelari chifukwa miseu yambiri idaonongeka kamba ka namondwe wa Freddy.

Pa nsamukowu, anthu akugwiritsa ntchito ngolo kunyamula katundu ndi kuoloka naye m’tsinje wa Ruo, nkukakweza mmagalimoto mbali ina ya delari.

Izinso zikupangitsa kuti a njinga akweze mitengo, poti anthu akumalipira K14,000 kupita ndi kubwera pa ulendo woyenda mwapendapenda chifukwa cha kuonongeka kwa miseu.

Poonetsetsa kuti ntchito yosamutsa anthuwa ikuyenda bwino, nthambi ya DoDMA inakumba mijigo mma gulupu onse asanu ndi anayi a m’delari omwe akusamuka, kukonza misewu, kupereka ndalama zosamutsira katundu wa sukulu ndi maanja, kumanga zipinda zophunzilira ndi nyumba za aphunzitsi zongoyembekezera, kupereka nthawira womwe ukugwiritsidwa ntchito ndi sukulu ya sekondale ya Makhanga yomwe inasamukila kumtunda.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.