Alimi achenjezedwa zogula feteleza wa manyowa pa nsika

Advertisement
Malawi organic fertilizer

Potsatira kukwera mtengo kwa feteleza wa mankhwala yemwe pano thumba lolemera 50 kilogalamu likugulitsidwa pa mtengo osachepera K90,000 m’malo ena, alimi achenjezedwa kuti asamalitse kwambiri akamagula feteleza opangidwa kuchokera ku manyowa yemwe ali mbwee m’misika pa mitengo yotsikirapo.

Ngakhale kuti dziko lino lilibe miyezo yoyenera yopangira feteleza kuchokera ku manyowa, malonda a feteleza wachilengedweyu afala kwambiri ndipo pano matumba okongola a fetelezayu alimbwelekete m’misika yochuluka m’dziko muno.

Ndizosachitaso kubisa kuti potsatira kusayenda bwino kwa nkhani za chuma m’dziko muno komaso kugwa kwa ndalama ya kwacha, alimi ang’onoang’ono ambiri afunitsitsa kuzemba mitengo yokwera ya feteleza wa mankhwala (chemical fertilizer), ndipo ina mwa njira yozembera mitengo yokwerayi ndikugwiritsa ntchito feteleza opangidwa kuchokera ku manyowayu.

Komatu paja chozemba chinakumana ndichokwawa. Akatswiri a zaulimi achenjeza alimi onse omwe akufuna kugula pansika ndi kugwiritsa ntchito feteleza opangidwa kuchokera ku manyowa, ponena kuti pali chiopsezo choti atha kubeledwa ndi atsizina mtole pogulitsidwa zinthu zomwe sifeteleza.

Katswiri wa zaulimi Dr Tamani Nkhono Mvula wati ngakhale feteleza wa manyowa ali wabwino kwambiri kugwiritsa ntchito paulimi, pali chiopsezo choti feteleza wa manyowa wambiri yemwe ali pansika atha kukhala osayenera kwenikweni kapenaso opanda michele yofunikira ku mbewu.

Dr Nkhono Mvula ati izi ndi kamba koti pakadali pano dziko lino lilibe mlingo ovomelezeka opangira fetelezayu (standards) zomwe a kuti zikupeleka kuthekera koti ena mwa ogulitsa feteleza wa manyowayu akhale ndi danga lopanga feteleza ochepa kapena opandilatu mphamvu ndi kumawagulitsa alimi.

“Vuto lomwe tili nalo pakadali pano ndi loti fetelezayu wambiri ngati siyese alibe chilolezo, ndiye n’kosavuta kuti alimi anyengedwe pa feteleza wa manyowayu, chifukwa ngati sadatsimikizidwe, nde kuti sadatengedwe ku labu kuti akatsimikizidwe, komanso kuwonetsetsa kuti kuchuluka kwa michere yomwe ili m’menemo ndi yovomerezeka, zomwe zikupereka chiopsezo cha chachikulu kwa alimi,” watelo Nkhono Mvula.

Pogwirizana ndi Dr Nkhono Mvula, katswiri winaso wa zaulimi Dr Kingdom Kwapata wati alimi omwe akukonzekera kugula feteleza wa chilengedweyu pamsika, ali pa chiopsezo chopusitsidwa kamba koti palibe ma satifiketi ndiye mlimi sangadziwe ngati zomwe wagulazo ndi fetelezadi weniweni.

Dr Kwapata alangiza alimi omwe akukonzekera kugula ndi kugwiritsa ntchito feteleza wachilengedweyu kuti awonetsetse kuti akugula kuchokera kwa ogulitsa odalirika komanso odziwika bwino ndicholinga choti ngati angakumane ndi vuto atagwiritsa ntchito fetelezayu, adzakathe kudandaula kwa yemwe anamugulayo.

“Opanga kapena anthu omwe akugulitsa feteleza wa manyowayu ayenera kukhala odalirika. Alimi ayenera kukhala ndi mbiri ya yemwe akuwagulitsa fetelezayu. Ngati alimiwo angapeze maumboni kwa ena omwe adagula ndi kugwiritsapo ntchito fetelezayu, zitha kukhalaso zabwino. Sitikufuna alimi abeledwe. Chifukwa ndizotheka kugulitsidwa zinthu zomwe sifeteleza, akuyenera kusamalitsa kwambiri akamagula,” achenjeza Dr Kwapata.

Iwo anapemphaso adindo kuti afulumizitse ntchito yopanga malamulo komaso mlingo wa kapangidwe ka feteleza wa chilengedweyu ndipo atsindika kuti ngati izi sizingachitike nsanga, alimi ochuluka omwe sangakwanitse kugula thumba la feteleza wa mankhwala, apitilira kudyeledwa ndalama ndi akathyali.

Posachedwapa nduna ya zamalimidwe a Sam Kawale, kudzera pa tsamba lawo la fesibuku, analimbikitsa alimi kupanga okha feteleza wa chilengedweyu pogwilitsa ntchito njira yotchedwa Mbeya.

Iwo anati pogwiritsa ntchito njira ya Mbeya, munthu amayenera kusakaniza 20 kilogalamu ya ndowe za nyama, 20kg ya madeya a chimanga, 10kg ya phulusa, 10 kilogalamu ya feteleza wamankhwala kenaka ndikuthiramo madzi ochuluka ma lita asanu.

Pambuyo pake, zosakanizidwazi zimayenera kutsanulidwa mu thumba lokhala ndi pepala la pulasitiki mkati, kusungidwa kwa masabata atatu ndipo kenako kuziumitsa pamthunzi.

Malingana ndi ndunayi, manyowa omwe asakanizidwa ndi feteleza wa mankhwala wa NPK, feteleza wachilengedwe opangidwayo amakhala okulitsa pomwe zosakanizidwa ndi fetelesa wa UREA, feteleza opangidwayo amakhala obeleketsa.

Advertisement