Bambo wa zaka 24 wamangidwa chifukwa chokupha mwana wa mlongo wake

Advertisement

A Phillip Mwanza a zaka 24 awamanga kwa Jenda ku Mzimba powaganizira kuti apha mwana wa mlongo wawo, a Steven Shaba, a zaka 21, ndewu itabuka kamba ka suti yovala pa ukwati

Mneneri wa Polisi ya Jenda a Macfarlane Mseteka ati izi zachitika dzulo ku Vibangalala m’bomali.

A Mseteka ati a Mwanza anapsa mtima kamba koti mlongo wawo adatenga ndi kuonetsa kwa anthu suti imene iwo adakonzekera kudzavala pa ukwati umene umayembekezeka kuchitika pa 28 october chaka chino.

Ndewu inabuka pakati pa Mwanza ndi mlongo wawo ndipo mwana wa mlongo wawoyo, a Steven Shaba, adalowelerapo kuti apulumutse mayi ake. 

Apa, a Mwanza adatenga mpini wa khasu ndi kumenya m’bale wawoyo amene adakomoka.

Shaba anathamangira naye ku chipatala cha Embangweni kumene adamwalira patangopita maola ochepa.

A Mwanza amangidwa ndipo akuyembekezeka kukayankha mulandu wakupha ku bwalo la milandu.

Iwo amachokera m’dera la Chikoko Manda, mfumu yaikulu Mzikubola ku Mzimba.

Advertisement