Lamulo ligwire ntchito pa aliyense posatengera kuti ndi ndani – Chakwera

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati aliyense amene akuchita zozunza anzake m’dziko muno lamulo ligwire ntchito pa iye.

Chakwera wayankhula izi pa mwambo wokhazikitsanso kampeni yothana ndi matenda a Cholera komanso Covid-19 ndinso matenda a nkhasa ya khomo la chiberekero omwe mchingerezi atchedwa Human Papilloma Vaccine (HPV) pa bwalo la Madimba m’boma la Likoma.

“Aliyense yemwe akuchita zozunza anzake ameneyo lamulo ligwire ntchito pa iye posatengera kuti ndi ndani,” watero Chakwera.

Mawuwa akudza pomwe a Lester Maganga, yemwe ndi wothandizira nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu, ali mchitokosi chifukwa choganiziridwa kuti anapha a Allan Wittika.

Mwa zina zomwe mtsogoleriyu anayankhula pa mwambowu ndi kufunika koti a Malawi azionetsetsa kuti akutsatira njira za ukhondo kuti apewe matenda a Cholera komanso Covid-19.

“Ife a Malawi tikuyenera kumasamba m’manja tikachoka kuchimbudzi, tisanaphike komanso tisanadye chakudya,” anaonjezera motero.

Chakwera walimbikitsanso asungwana a zaka zapakati pa 9 mpaka 14 kuti akabaitse katemera othana ndi nthenda ya khansa ya khomo la chiberekero -HPV mzipatala zomwe ali nazo pafupi.

Pa mwambowu mtsogoleri wa dziko linoyu anapereka ma ambulance koma njinga za kapalasa zomwe zigawidwe m’madera ena mdziko muno ndi cholinga chopititsa patsogolo ntchito za umoyo.

Advertisement