Chakwera akawonelera kukolora tirigu ku Dowa

Advertisement
Pyxus Farm in Madisi in Malawi

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera mawa lachisanu akhala ali m’boma la Dowa komwe akawonelere kukolora koyamba kwa Tirigu pa munda wina kenaka akukakhazikitsa ndondomeko ya fetereza wotchipa ku Kasungu.

Izi ndi malingana chikalata chomwe boma latulutsa chomwe wasayinira ndi mlembi wa mkulu wa boma mayi Colleen Zamba.

Mayi Zamba munkalatayi ati mtsogoleri wadzikoyu akakhala akuwonelera kukolora koyamba kwa tirigu pa munda wa Mpale kwa mfumu yaikulu Chakhaza ku Dowa.

Iwo ati a Chakwera akakachoka ku Dowa akakhala akulowera ku Kasungu komwe kukakhale mwambo okhazikitsa ndondomeko ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo.

Mwambo okhazikitsa ndondomeko ya Affordable Input Program (AIP) ya chaka chino, ukuyembekezeka kukachitikira pa bwalo la zamasewero la Kavidebwere pulaimale kwa mfumu yaikulu Kaluluma ku Kasungu.

“Olemekezeka Dr. Lazarus McCarthy Chakwera, mtsogoleri wa dziko la Malawi mawa, Lachisanu pa 20 October 2023:

“Akawonelera kukolola koyamba kwa tirigu ku Mpale Wheat Farm-Pyxus Agriculture, dera la mfumu yaikulu Chakhaza, Dowa:

“Ndi kukhazikitsa ndondomeko ya Affordable Input Program (AIP) pa bwalo la masewero la sukulu ya Kavidebwere, dera la mfumu yaikulu Kaluluma, Kasungu,” yatelo kalata ya boma yomwe inalembedwa mchizungu.

Advertisement