Kusowa kwa mafuta kwakhudzanso boma la Salima

Advertisement
Public transport fares have gone up in Malawi following shortage of fuel in the country

Kusowa kwa mafuta agalimoto kwakhudza nkhani ya mayendedwe m’boma la Salima pamene mitengo yokwerela magalimoto yakwera.

“Kuchoka pa Kamuzu Road kupita pa Golomoti tsopano ndi K5,000 kuyerekeza ndipamene mafuta akakhala kuti akupezeka timachita K3,500,” M’modzi mwawoyendetsa magalimoto pa Kamuzu Road anayankhulana ndi Malawi24 m’mawa uno.

Nawo ochita malonda m’bomali omwe amadalira maulendo apa msewu ati ndi odandaula kamba kavutoli kotero apempha boma kuti lichitepo machawi kukonza vutoli.

Tsopano papita masiku atatu m’boma la Salima pamene malo omwetsera mafuta akadali chuu chiumire kamba kavutoli

Wolemba: Ben Bongololo, Salima

Advertisement