Anthu 15 amangidwa chifukwa chowononga katundu wa ndalama zokwana K23 miliyoni

Advertisement

Apolisi m’boma la Chiradzulu amanga anthu okwana 15 ochokela m’mudzi wa Chitera powaganizila kuti aphwanya ndi kuba katundu wa ndalama zopitilira 23 miliyoni kwacha pa Chikale esiteti yomwe ndi ya Mulli Brothers.

Malinga ndi mneneri wa a polisi ku Chiradzulu a Cosmas Kagulo, anthuwa anachita izi pokwiya ndi poganiza kuti mzawo wina anamangidwa chifukwa cha esitetiyi.

Koma malingana ndi a Kagulo, iwo ati munthuyu anamangidwa pa nkhani ina yokhudza umbanda.

“Munthuyu atamangidwa, anthu a m’mudzimo anayamba kugenda komanso kuba ku esitetiku poganiza kuti munthuyu wamangidwa chifukwa cha kampaniyi pamene sizinali choncho,” adatero a Kagulo.

Anthuwa akuganizilidwa kuti aphwanya nyumba ndi kuba 500 sauzande komanso mota yachigayo ndipo oganizilidwawa akuyembekezeleka kukaonekela kubwalo la milandu kafukufuku akafika kumapeto.

Olemba Andrew Salima

Advertisement