Anthu m’masamba anchezo akugawana kanema ya oyimba Napier ‘ Nepman’ Longwe yomwe anamasuka ndikuwulura kuti luso lothyakula nyimbo lomwe ali nalo silimubweretsera ndalama zoti angadyetse banja lake kuyelekeza ndi bizinezi ya iligo yomwe akuti amapanga.
Nepman yemwe amakhala munzinda wa Blantyre, anayankhula izi pa 18 August chaka chino nkatikati mwa kucheza kwake mu pologalamu ya Streethouse pa kanema wa pa intaneti wa Crafthouse.
Mukulongosora kwake, chiyamba kale pa mayimbidweyu anati kuyimba kwa iye kulibe phindu kwenikweni ndipo wati ndi chifukwa chaka m’chaka cha 2021 anabwera poyera ndikulengeza kuti wazituluka za mayimbidwe.
Apa Nepman yemwe ndi mwini wake wa nyimbo yotchuka ya ‘Nalero’ anati anabweleraso m’mayimbidwe kamba koti anthu ena omwe amakonda nyimbo zake anamufikira ndikumunyengelera kuti asasiye kuyimba.
Oyimbayu anati ngakhale zili choncho, kuyimba kumamuwonongera ndalama zochuluka zedi poyelekeza ndi phindu lomwe amalipeza ndipo wati amayimbabe chifukwa choti pano anazindikira kuti ndimayitanidwe ake.
“Kunyimbo kumapezekabe tinatake komano tili ndi njira zina zimene timapanga kupatula nyimbo, ndi zimene ndimadalira kuposaso kuimba nyimbo. Chifukwa kuimba makamaka kwa ineyo kumandionongera ndalama zambiri. Panopa kukaimba nyimbo imodzi yokha ndi K70, 000 kapena K80,000, mtengo uwuwu ndiwa nyimbo yovera basi.
“Nanga tikati nyimboyo tiyijambule yowonera. Komaso pamenepa sitinaikepo ndalama ya mayendedwe, palibeposo ndalama ya chakudya. Kupatula apo ineyo ndi munthu amene ndimafuna kuti ndisanaimbe ndimwe kaye kachakumwa kena kake. Nde kuti ndijambule nyimbo yowonera pakufunika pafupifupi K500,000. Apa zikusonyeza kuti chinthuchi timangopanga chifukwa choti chili mkati mwathu,” anatelo Nepman.
Chomwe chadzetsa tsemwe anthu ambiri ndimomwe Nepman anayankhira mwaukadziwotche fuso lomwe anafusidwa kuti atambasule zomwe amatanthauza pa mawu ake onena kuti ali ndi njira zina zopezera ndalama osati mayimbidwe.
Apa ndi pomwe mkuluyu m’maso muli mbee, komaso mosapsatira anawulura kuti amachita ma bizinezi osavomelezeka (illegal) omwe wati ndi omwe amamuthandizira kusamalira nthiti yake komaso ana ake.
Oyimbayu anamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sangaulure ma bizinezi a iligo omwe akuti amapangawo ponena kuti dzikoli silikuyenda bwino, nde kuwulura sizingamuchitire ubwino.
“Pali zambiri, ndinapanga za maphikidwe (catering), nde paliso tima iligo (illegal) bizinezi toti sindingatinene mapeto ake sinanga ndi dzikoli m’mene lilili sizigwira. Sindingaulule chifukwa ndalama zanga ndimazipeza kumenekoko.
“Za nyimbo sindingadalire, zimene zimandibweretsera ndalama zambiri panopa kwa ineyo ndi izizi za iligozi kuposaso kuyimba nyimbo, nde sindingakambeso kuti iligo yake ndi iyi ndi iyi. Nkhani tiyeni tikambe za maimbidwezi, izizi zisiyeni ndi zimene zikudyetsa banja langa, makolo anga ndi azibale anga,” anateloso Nepman.
Pakadali pano anthu ena pa fesibuku akudzudzula oyimbayu kamba ka zomwe anayankhulazi ponena kuti zili ndi kuthekera komubweletsera mavuto.