Amapanga chiganizocho kapena adaledzera? – yadabwa Wanderers

Advertisement
Chancy Gondwe is a lawyer and a football administrator in Malawi

…yati ikuwunika kuti apange apilu kapena ituluke zikho zonse

Timu ya mpira wa miyendo ya Mighty Mukuru Wanderers yati iwunikira kuti ipeze ngati omwe anapanga chigamulo chawo analawa nkalabongo kapena ayi, ndipo yati ikudziwa ma timu omwe akuluakulu omwe apanga chigamulochi amasapota.

Izi ndi malingana ndi a Chancy Gondwe omwe ndi mlembi wankulu wa bodi yatimu ya Mighty Mukuru Wanderers omwe anayankhula ndi nyumba zina zofalitsira mawu m’dziko muno.

Iwo amayankhula izi kutsatira chigamulo chomwe bungwe loyendetsa mpira m’dziko muno la Football Association of Malawi (FAM) lapeleka potsatira zipolowe zomwe zinachitika loweluka sabata yatha pomwe timuyi imasewera ndi Silver Strikers ku Lilongwe mumpikisano wa Airtel Top 8.

A Gondwe anatsimikiza kuti chigamulo cha FAM chawapeza ndipo akuchiwerenga kaye koma ati sakudabwa kalikonse ponena kuti anali akudziwa kale kuti zinthu zikhala choncho.

Iwo anati kusadabwako ndi kamba koti timu yawo ikudziwa bwino lomwe anthu omwe ali mukomiti yosungitsa mwamba ku bungwe la FAM, komaso ati akudziwa ma timu omwe akuluakulu osungitsa mwambowo amasapota.

“Yaa tachilandira bwino ndithu chiganizo chimenecho ndipo tikudziwa bwino anthu amene ali mu komitiyo, tikudziwa matimu amene amasapota. Ifeyo tinakozekera kale kuti chiganizo chawo chikhala chonchi, nde chiganizo amafuna kupangacho achipanga, tachilandira.

“Ife tichiwunika chiganizochi bwino bwino; kaya tichita apilu (appeal), kaya sitichita apilu, kaya tituluka mmipikisano yonse m’dziko muno, tipanga chiganizo ndipo chiganizo chimenecho tidzanena kudzera mwa anthu oyenera kuti ichi nde chiganizo chomwe chapangidwa ndi timu ya Mighty Wanderers,” anatelo a Gondwe

Iwo atsindika kuti posachedwapa akhala akubweraso poyera kuliuza dziko za maganizo a timu yawo pa chigamulo cha FAM ndipo ati akufuna awunike bwino bwino kuti omwe anapanga chigamulochi anapanga ataledzera kapena ayi.

“Kwa pano tikuyang’ana, tikuwerenga chigamulo chimenechi kuti amapangawo analedzera kapena anapanga chiganizochi bwino bwino. Nde tichiunika, tifusana fusana kenaka tidzanena kuti tapanga chiganizo ichi,” anawonjezera a Gondwe.

Mpungwepungwe udabuka mu nthawi yowonjezera pomwe Stein Dave anamenyera mpira mu ukonde pa nthawi yomwe oyimbira Godfrey Nkhakananga anayimba kherere kuti mpira uyime kaye ndipo kenaka oyimbira yemweyo anasintha chiganizo ndikuvomera chigolicho.

Masewerawa omwe pa nthawiyi anali pa 2:2, anathera pa njira kamba koti timu ya Wanderers inakanitsitsa kuti siyipitiriza kusewera pokhapokha Nkhakananga abwezeretse chiganizo chake choyamba choyimba wenzulo kuti mpira uyime kaye koma nayeso anakanitsitsa.

Izi zinapangitsa ochemelera omwe akuganizilidwa kuti ndi a timu ya Wanderers yomwe oyikonda amangoti Noma, kuyamba kuchita chisawawa ndipo mwa zina, anathyola mipando ya pa bwalo la Bingu.

Ndipo muchigamulo chaka, FAM yapeza yolakwa timu ya Wanderers yomwe ayigamura kuti inaluza masewerowa 2:0 komaso yauzidwa kupeleka chindapusa cha ndalama zokwana K24.5 miliyoni yomwe akuti igwira ntchito yokozera zomwe zinawonongekazo

Pakadali pano mkulu oyang’anira bwalo la Bingu Ambilike Mwaungulu, ati mipando 70 ndi yomwe inaonongedwa ndipo wati ndalama zosachepera K10 million ndi zomwe zingafunikire kubwezeletsa mipandoyi.

Advertisement