Ochita kabaza ku Salima asimba lokoma

Advertisement

Anthu ochita kabaza wanjinga zamoto m’boma la Salima, tsopano akhala akusimba lokoma pamene bungwe loona za pamsewu la Directorate of Road Traffic and Safety Services likhale likupereka ziphaso zoyendera pamsewu za ochita kabazawa.

Poyankhulana ndi Malawi24, ena mwaochita kabazayu ati iwo ndiwosangalala kamba kaganizoli chifukwa zithandiza kuti apeze chiphaso choyendera pamsewu mosavuta.

M’modzi mwawogwira ntchito ku Malawi Road Traffic yemwe anali nawo pa ranki yanjinga zamoto pa Kamuzu Road m’boma la Salima, anafotokoza kuti ziphaso zoyendera pamsewuzi zikhale zikuperekedwa kudzera mupologalamu ya Mobile MaLTIS.

A Malawi Road Traffic anali m’boma la Salima paulendo wawo odziwitsa anthu za pologalamu ya Mobile MaLTIS komanso kuwaunikira ochita kabaza wanjinga zamoto ubwino olembetsa njinga zawo.

(Wolemba, Ben Bongololo, Salima)

Advertisement