Mnyamata wa zaka 18 waphedwa ku Balaka

Advertisement

Apolisi ku Balaka akusaka anthu amene anapha mnyamata wa zaka 18, Gift Libuda, yemwe anali mu folomu 3 pa sukulu ya St Charles Lwangwa Secondary.

Malingana ndi mneneri wa Police m’bomali a Gladson M’bumpha, mnyamatayu anachoka kwawo lamulungu pa 10 September, 2023.

Iye anapita kwa agogo ake kwa Chiyendausiku kuti akatenge katundu wina pokonzekela kutsegulira kwa sukulu.

Atafika pa malo omwetsela mafuta a Ngwangwa, anakwera galimoto la mtundu wa Sienta mmene anapezamo anthu ena awiri ndi oyendetsa.

Dalaiva was galimotoyi anauza anthuwo kuti akufuna akatenge anthu ena pa Andiamo koma atafika pa Andiamo, anthu ena awiriwo anamugwira Gift pakhosi ndikumumwetsa zinthu zosadziwika kenaka anamumenya.

Iwo anamusiya Gift atakomoka pa Malo omwewo.

Gift atatsitsimuka anafika panyumba ya Rajab Maliro pamene anapeza malo ogona.

Mam’mawa wake eni nyumbayi anamupeza Gift atafooka kwambiri ndipo Gift anafotokoza zomwe zinamuchitikira.

A Maliro anauza makolo ake za izi, ndipo Gift anatengedwa ku polisi kenaka ku chipatala cha Balaka kumene anamwalira akulandira chithandizo.

Gift amachokera mmudzi mwa Kaumphawi, mfumu yayikulu Nsamala m’bomali.

Advertisement