Boma lalamula MACRA kuchotsa chiletso pa mitengo yatsopano ya DStv

Advertisement
Moses Kunkuyu information minister Malawi

Boma kudzera kuunduna wa zofalitsa nkhani walamula bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) kuti lichotse chiletso choletsa kampani ya Multichoice Africa Holdings kukweza mitengo ya DStv.

Nkhaniyi inayamba pa 21 July, 2023 pomwe kampani ya Multichoice kudzera pa masamba ake anchezo, inalengeza kuti kuyambira pa 1 August chaka chino, mitengo yomwe makasitomala amapeleka pogula ma pakeji osiyanasiyana pa DStv, ikwera.

Malingana ndi Multichoice, pakeji yotchipitsitsa yomwe imatchedwa Kufewa, ikuyenera kulipilidwa K7,500 kuchoka pa k6,800 pomwe yotsatilana nayo ya Access yachoka pa K10,200 kufika pa K12,500 ndipo pakeji ya Family yafika pa pa K19,500 kuchoka pa K16,400 pamwezi.

Mbali inayi, pakeji ya DStv yotchedwa Compact tsopano yachoka pa K27,500 kufika pa K33,000 pamene Compact Plus yachoka pa K43,000 kufika pa k51,000 ndipo mtengo wa pakeji ya Premium wachoka pa K67,000 kufika pa K79,000 pa mwezi.

Kukweza mitengoku sikunasangalatse bungwe la MACRA lomwe linakatenga chiletso ku bwalo la milandu choletsa kampani ya Multichoice kukweza mitengo ya mapakeji onse a DStv.

Kutengedwa kwa chiletsoku kunapangitsa kuti kampani ya Multichoice ilengeze kuti isiya kupeleka ma sevisi a DStv m’dziko muno.

Ndipo polowelerapo pa nkhaniyi, boma la Malawi kudzera ku unduna wazofalitsa nkhani lachinayi pa 24 August, 2023, walamura bungwe la MACRA kuti lichotse chiletso chomwe linatengachi.

Undunawu wati ngakhale ukudziwa bwino kuti bungwe la MACRA ndiloyima palokha, koma pomwe yafika nkhaniyi mpoyenera kuti bungweli litengeko upangili kuchokera ku unduna wa zofalitsa nkhaniwu.

“Choncho ndikulamura MACRA kuchitapo kanthu mwachangu kuti ibwezeretse zomwe zidalipo kale isanakatenge chiletso ndicholinga choti nkhaniyi ithetsedwe mwansanga komaso kunja kwa bwalo la milandu,” yatelo mbali ina ya chikalatachi chomwe wasainira ndi nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu.

Pakadali pano bungwe la MACRA silinayankhulepo kanthu za nkhani koma zokambirana zofuna kuva maganizo mbali zonse zokhudzidwa zikuyenera kupitilira mawa.

Advertisement