Mayi waotcha nyumba ya bwenzi lake ku Kasungu

Advertisement
Fire incident Kasungu

Mayi wa zaka 26 yemwe dzina lake ndi Omega Pemba ali m’manja mwa apolisi ku Kasungu chifukwa chotentha nyumba ya bwenzi lake ndikuwononga katundu wa ndalama zokwana K7.9 miliyoni.

Mayiyu adachita izi dzana pa, 15 August, m’mudzi mwa Nkhoma kwa mfumu yayikulu Nyaza ku Kasungu

Mneneri wapolisi m’boma la Kasungu a Joseph Kachikho wati Pemba ndi bwenzi lake Blessings Chikapa adasemphana maganizo.

Akuluakulu ena adalawelerapo ndikuweruza nkhani yawoyi koma Pemba sadagwirizane ndi m’mene akuluakuluwa adaweruzira nkhaniyi.

Nthawi ya 11:30 usiku pa 15 August mayiyu adayatsa nyumba ya Chikapa ndipo moto udayendelera mpaka kuotcha katundu okwana K7.9 miliyoni.

Nkhaniyi idakaperekedwa ku polisi ndipo Pemba adamangidwa.

Mayi oganiziridwayo amachokera m’mudzi mwa Ndewu mfumu yayikulu Kayembe m’boma la Dowa ndipo akayankha mlandu otentha nyumba ndi katundu.

Advertisement