Anthu ayamba kulozerana nyumba ya malemu Goodall Gondwe

Advertisement
House of Goodall Gondwe Malawi

Nanga inu adzalozerana chiyani mukadzatsamaya? Ndalama osamangodya ngati kuti ndi tomato yemwe mukuopa kuti awola mukakhalitsa naye: anthu uku atutumuka ndi chinyumba cha malemu Goodall Gondwe, ndipo kuli kulozerana kwinaku akuomba m’manja kuti Phuu! Kuli kusavetsetsa ndi zomwe apenya.

Anthu ochuluka tchimo lomwe ali nalo ndilosakumbuka kumanga nyumba zokhalamo; osangoti nyumba wamba koma nyumba zomwe zitha kumapeleka kaso kwa anthu ndipo owonayo atha kulozera nzake kuti tawona nyumba iyo bwanawe.

Tchimo losamanga nyumba limaonekera kwambiri pomwe pa mudzi pagwa zovuta ndipo nthawi iyi ndi yomwe abwenzi amadzionera okha zakuchenjera kapena kumbwambwana kwa nzawo yemwe akumukhazikayo kapena womwalirayo.

Anthu ambiri akamakhala m’ntauni, amakomedwa ndi nyumba zobwereka kuyiwala kuti tsiku lina thupi lawo lidzafuna malo ogonekedwa ku mpanje kwawo ndipo khamu la anthu lidzafuna pokhala poyembekesera kuwapelekeza kumalo achetewo.

Komatu izi sizinali choncho ndi malemu Goodall omwe apeleka chitsanzo chabwino chogwiritsa bwino ntchito makopala omwe ankapeza ali moyo pomanga nyumba yomwe anthu akulephera kusimba.

Chithuzi cha nyumba ya malemu Gondwe chikuzungulira m’masamba a nchezo ambiri ndipo anthu ochuluka akusilira kaamba ka kukula kwake komaso mamangidwe amtengo wapataliwo.

Malingana ndi zithuzi zomwe tsamba lino lawona, munthu yemwe ndikoyamba kuwona chomangidwacho atha kumaona ngati ndi malo odyera komaso kugonera alendo kamba koti inamangidwa mochititsa kaso zedi.

Mtheradi chuluke chuluke mngwa njuchi, nyumba ya malemu Gondwe yadulitsa mitu yazizwa ndipo anthu akuti ichi chikhale chitsanzo kwa anthu ochita andale komaso ma khumutcha onse m’dziko muno kuti ndalama osamangoyika pa lilime.

“Chinyumba Cha Malemu Goodall Gondwe. Big lesson to us (phunziro lalikulu kwaife). We need to learn to invest when we are alive and strong (tikuyenera kuphunzira ku sunga ndalama tinakali moyo komaso a mphamvu,” watelo munthu wina pa fesibuku poyikira mlomo za nyumba yo.

“Anthu azizimuka ndi nyumba ya nduna yakale yaza chuma malemu Goodall Gondwe. Akufusana anthu kuti imeneyi nyumba yogonamo kapena multi purpose Hall?” Wadabwaso munthu wina pa fesibuku.

Podziwa kuti pagulu sipamalephera anthu othira nchenga mu mpunga wa gulu, anthu ena a kuti chodandaulitsa nchoti ngakhale mkuluyu anamanga nyumba ya pamwamba, koma wayisiya ndikupita ku malembe, maloosapeleka chidwi, malo olilitsa.

“Ichi ndi Chinyumba cha a Goodall Gondwe omwe amwalila aja, Chinyumbatu kuposa hotel, tikamakhala tizikumbukila kuti Mlaliki anati za dziko nzachabe ndipo zongosautsa mtima, zithu zosenzi,” latelo tsamba la Ndizaulula pa fesibuku.

A Goodall Gondwe omwe amwalira lachiwiri sabata ino, anali Katswiri pa zachuma ndipo adakhalapo nduna ya yoona zachuma m’dziko muno komaso atisiya ali wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha DPP mchigawo chakumpoto.

Malemuwa omwe amwalira ali ndi zaka 87, anali ochokera m’mudzi wa Kayiwononga ku Enukweni, mfumu yaikulu Mtwalo m’boma la Mzimba komweso thupi lawo likuyembekezeka kolowa m’manda la mulungu pa 13 August, 2023.

Advertisement