Bungwe la MEC lati kugwiritsa ntchito zipangizo za boma pa misonkhano ya ndale ndikosaloledwa

Advertisement

Bungwe lowona za chisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lati kugwiritsa ntchito zipangizo za boma monga galimoto pamisonkhano ya ndale yokopa anthu pachisankho ndikosaloledwa ndipo bungweli lati aliyense opezeka akuchita izi adzayimbidwa mlandu.

M’modzi mwa makomishonala a MEC a Richard Chapweteka ndi womwe ayankhula izi mu mzinda wa Zomba pomwe amafotokozera atolankhani za ndondomeko yamalamulo achisankho chikubwerachi.

A Chapweteka ati anthu monga akuluakulu oyang’anira nthambi za boma komanso nduna ndiwosaloledwa kugwiritsa ntchito zipangizo za boma monga galimoto pamisonkhano ya ndale kupatula.

Koma iwo anati malamulowa sakukhudza pulezidenti ndi wachiwiri wake.

Iwo adatinso wandale aliyense yemwe adzapezeke akunyoza kapena kuyankhula mau osayenera kwa nzake yemwe akupikisana naye nthawi yamisonkhano yokopa anthu adzayimbidwa mulandu.

“Pofuna kuti misonkhano yokopa anthu idzakhale ya bata ndi mtendere malamulo akuletsa kuchita misonkhano yonyozana kapena kuyankhula mawu okuti nzathu yemwe tikupikitsana naye amve kuwawa mumtima,” adatero komishonala Chapweteka.

Pamenepa a Chapweteka adatinso malamulo a chisankho akunena kuti nthawi yoponyera chisankho idzayamba 6 koloko mam’mawa kulekeza 4 koloko madzulo kusiyana ndi m’mbuyomu pomwe kuponya voti kumayamba 6 koloko mam’mawa mpaka 6 koloko madzulo pofuna kuti kuwerenga ma voti kudzayambe nthawi yabwino.

Iwo adafotokozeranso atolankhani kuti pachisankho cha chaka cha 2025 zipani zikupemphedwa kudzasankha munthu yemwe ali ndi digili kuti adzakhale komishonala wa bungwe lowona zachisankho la MEC.

Bungwe la MEC likuyembekedzeka kudzachititsa chisankho chosankha mtsogoleri wadziko, aphungu akunyumba ya malamulo komanso ma khansala mu chaka cha 2025.

Advertisement