Khonsolo ya boma la Lilongwe yati igwiritsa ntchito ndalama yokwana K2.5 miliyoni ya misonkho ya a Malawi pa ntchito yozula pholo la mbendera ndikukaliyika pa malo ena ku ma ofesi kwawo komweko.
Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe tsamba lino lawona chomwe chikuzungulira mmasamba a nchezo chomwe chikufotokoza mmene ndalama zigwilitsidwile pa ntchito yonseyi.
Chikalatachi chikusonyeza kuti gawo lokozekera, lomwe ndikupeza kontalakita (contractor) yemwe agwire ntchito yosamutsa phololi, igwiritsa ntchito ndalama yokwana K800,000.
Kuchoka apo, gawo la chiwiri la ntchito yozula pholo la mbendelali ndikukaliyika pa malo atsopano omwe akufunidwawo, akuti itenga ndalama za misonkho ya a Malawi zokwana K1,623,000.
Khonsoloyi yatiso ndalama yokwana K27,000 igwira ntchito mu gawo lachitatu la ntchitoyi yomwe akuti ndi kusamalira ngalande pamalowa, kuyiyeletsa kuti iwoneke mopatsa chikoka.
Pakadali pano anthu osiyanasiyana m’dziko muno kuphatikizapo akatswiri azachuma, akudzudzula khonsoloyi kaamba kosalabadira kusamala ndalama za dziko lino.
Anthu ena ati nzodabwitsa kuti m’dziko losauka pazachuma ngati Malawi ndalama zochuluka chonchi zomwe ndi misonkho ya a Malawi, zitha kuwonongedwera pazinthu zosafunika kwenikweni ngati pholo la mbendelali.
Correction: The earlier version of the story incorrectly referred to Lilongwe City Council instead of Lilongwe District Council. We apologise for any inconvenience caused by this mistake.
M’kati mwa nkhaniyi tinatchula kuti khonsolo ya mzinda wa Lilongwe ikufuna kugwiritsa ntchito K2.5 miliyoni kusamutsira pa malo ena pholo la mbendera. Apa tinalakwitsa. Ndi khonsolo ya boma la Lilongwe (Lilongwe District Council) imene ikufuna kuwononga ndalama zankhaninkhanizi osati khonsolo ya mzinda wa Lilongwe (Lilongwe City Council). Tikupepesa ku khonsolo ya mzinda wa Lilongwe chifukwa chakulakwitsa kwathu.