Sindikukwatiwa pano – Tabitha Chawinga

Advertisement

Tabitha Chawinga yemwe ndi katswiri posewera mpira wa miyendo wati iye adzayamba kuganiza zokwatiwa akadzafika zaka makumi atatu (30).

Chawinga yemweso ndi mtsogoleri wa osewera mpira wa miyendo ya atsikana ya dziko lino ya Scorchers, amayankhula izi pomwe amacheza ndi wailesi ya Malawi Broadcasting Corporation (MBC).

Osewerayu yemwe posachedwepa wakhala mtsikana oyamba mu Africa kumwetsa zigoli zambiri mumpikisano wa m’dziko la Italy komwe amasewera mu timu ya Inter Milan, wati alibe maganizo okhazikika pa banja pakadali pano.

Iye wati chomwe akuchita pano ndikulimbikira kusewera mpira womwe akuti ndi omwe akuona kuti ungamuthandize kukwanilitsa maloto ake.

Katswiriyu yemwe ali ndi zaka 27 wauza MBC kuti ndi zomvetsa chisoni kuti kulikonse komwe amapita anthu amamufunsa kuti akwatiwa liti ndipo wati kukwatiwa kapena kukwatira nsanga kumabweretsa umphawi.

“Ndizomvetsa chisoni kuti atsikana ambiri m’dziko muno amakwatiwa ndikubereka ali aang’ono azaka 15, 16, 17, ndizachionekere kuti ana otere sangathe kusamalira ana awo motero amakakamiza boma kuti litelo. Ndidzayamba kuganiza zokwatiwa ndikadzakwanitsa zaka 30,” watelo Chawinga.

Iye walimbikitsa achisodzera m’dziko muno kuti aziyika patsogolo maphunziro kapena maluso omwe ali nawo osati kuthamangira kukwatiwa kapena kukwatira.

Chawinga ali m’dziko muno kutchuthi ndipo ma timu akuluakulu ambiri akunja akupitilira kuwonetsa chidwi chofuna kulemba ntchito yosewera mpira katswiri ogoletsa zigoliyu.

Follow us on Twitter:

Advertisement