Mtsogoleri wakale wa chipani cha United Democratic Front (UDF) Atupele Muluzi, wati dziko lino litakhala ndi utsogoleri wabwino litha kufika pomwe anafika mayiko a Dubai, Kuwait ndi Qatar pa zaka khumi zokha osati kudikira mpaka 2063 komwe ati ndikutali kwambiri.
A Muluzi amayankhula izi lamulungu pa 11 June, 2023 pabwalo la masewero la Masintha mumzinda wa Lilongwe pomwe chipani cha UDF chimasangalala kuti chatha zaka makumi atatu (30) chikhazikitsidwile m’dziko muno.
Poyankhula ku khwimbi la anthu lomwe linasonkhana pa malowa, a Muluzi ananyalapsa masomphenya a boma oti dziko lino lidzakhale pamlingo wa pakati pankhani za chuma pofika mchaka cha 2063, ponena kuti 2063 ndikutali kwambiri.
Apa iwo anati dziko la Malawi lili ndikuthekera kwakukulu kotukuka kwambiri pa chuma ndi kufika pa mlingo omwe anafika mayiko monga China, Bahrain, Kuwait pasanathe zaka khumi osati kidikira mpaka 2063.
Mkuluyu anati dziko la Malawi lili ndi zinthu za chilengedwe zochuluka monga gasi, mafuta, madzi, mitengo ndi miyala yamtengo wapatali yomwe ingagwiritsidwe ntchito kulitukula pa chuma.. ,
“2063 ndikutali kwambiri, ena mwaife mwina Mulungu satisunga kufika kumeneko, ndikutali kwambiri. Mu nthawi yochepa osapitilira zaka khumi tikhoza kukhala pa mlingo ya Dubai, Qatar komaso Kuwait. Ndizotheka koma tiyenera tibwera pamodzi,” watelo Muluzi.
Iye anapitilira kunena kuti dziko la Malawi linakakhala litalemera kalekale koma vuto atsogoleri ake samapeleka mayankho ku mavuto omwe anthu akukumana nawo.
A Muluzi omwe ndi mwana wa mtsogoleri wa kale wa dziko lino, Bakili Muluzi, anatiso China so chomwe chabwezeretsa m’mbuyo dziko lino pa chitukuko, ndi kukula kwa mchitidwe wa katangale komwe akuti kwafika pa mwana wakana phala.
“Vuto limene tili nalo m’dziko muno ndi utsogoleri. Ntchito ya mtsogoleri ndikupeza njira zothetsera mavuto omwe tikukumana nawo osati kubwera ndikumatiuzaso mavuto omwe tikuwadziwa kale.
“Vuto lina lomwe lakula ndi kuba. Dziko la Malawi ndi lolemera kwambiri koma vuto atsogoleri tikatenga boma situkuwaganizira anthu, tikamakhala tikungoganiza kuti tisolora zingati, ngati muli katangale m’dziko sitingapite patsogolo,” anateloso Muluzi.
A Muluzi anapitilira ndikupeleka chiyembekezo kwa a Malawi ponena kuti iwo akugwirizana ndi katswiri wa za chuma waku Iran yemwe adathandizira dziko la China kuti lisinthe kuchoka paumphawi wadzaoneni kufika pomwe lili pano.
Iwo ati mgwirizano wawo ndi katswiriyu, a Farzam Kamalabadi, uthandiza kuti dziko lino lipeze njira zopezera ndalama yokwana 1 thililiyoni za m’dziko la America (one trillion USD) kuchokera ku zachilengedwe zomwe dziko lino lili nazo.
Iwo ati ndalama zotukulira dziko linozi zidzakhala mu thumba lotchedwa Sovereign Wealth Fund ndipo ati izi ayamba kuchita pano osati kudikira kudzalowa m’boma pa chisankho chomwe chikubwera mchaka cha 2025.
“Izi ndikukambazi sikuti tiyamba tikalowa m’boma 2025, tiyambe pano. Nthawi ya mtsutso ndinkanena kuti vuto atsogoleri timangolankhula zinthu osachita, koma ine ndi amzanga tiyamba, muwone nokha. Masiku akubwerawa tikumana ndi National Planning Commission ndi ena kuti tiyambe kumanga Malawi wa tsopano. Ntchito yanga ndikupeza mayankho ku mavuto anu,” anateloso Muluzi.
Polankhula pa msonkhanowo, mtsogoleri wa chipani cha UDF, Lilian Patel, wanenetsa kuti chipanichi chomwe chinali chipani cholamula pakati pa zaka za 1994 ndi 2006, chilowaso m’boma mu 2025.
“Tidzawadabwitsa mu 2025 titapambananso titapambanaso mipando yambiri mchigawo chapakati,” anatelo Patel.
A Patel anaonjeza kuti zokonzekera za msonkhano waukulu wa chipani cha UDF komweso kukakhale kusankha maudindo kuphatikiza kusankha mtsogoleri wa chipanichi kuli mkati ndipo walangiza mamembala kuti asatenge msonkhano wawowu ngati chida chogawa chipanichi.
Follow us on Twitter: