Vera wa zaka 10 ku Balaka akufunika thandizo la njinga yoyendera anthu a ulumali

Advertisement

Vera Kadwale wa zaka 10 yemwe amachokera m’mudzi wa Ngomano, Mfumu yaikulu Chimatiro  M’boma la Balaka ndipo salankhula komanso kuyenda akufunika thandizo la njinga yoyendera anthu a ulumali.

Vera akukanika akusangalala ndi maufulu osiyanasiyana omwe ana anzake amakhala nawo monga  ufulu wa maphunziro ndi kusewera kamba kosowa njinga yoyendera anthu a ulumali.

Vera, yemwe ali ndi zaka zakubadwa khumi adakumana ndi ulumali patangotha miyezi isanu ndi itatu chibadwireni.

Mwanayu samatha kulankhula komanso kukhala pansi ndipo nthawi zonse amakhala chogona pa mphasa.

Malingana ndi a Mercy Lobeni omwe ndi mai ake a mwanayu, akuti adawawuzidwa kuti vutoli lidayamba chifukwa cha  nthenda ya malungo aakulu, yomwe idathamangira mu ubongo.

A Lobeni omwe ali ndi zaka zakubadwa makumi anayi ndi zitatu komanso ali ndi ana asanu ndi m’modzi, adawuza Malawi24 kuti ayendapo mu zipatala zosiyanasiyana kusaka thandizo koma izi sizidaphule kanthu.

”Ndayenda naye mu zipatala za kuno ku Balaka komanso ku Liwonde koma palibe chomwe chidasintha. Padakalipano ndikulephera kupitiliza kusaka thandizo mu zipatala malingana ndi vuto la umphawi,”  adafokotokoza a Lobeni.

Maiwa adati akukumana ndi mavuto adzaoneni potengelanso kuti alibenso wina yemwe angawagwire dzanja poeza bambo amwanayo nawonso adathawa atadziwa za ulumali wa mwanayo ndipo pano sakudziwika kuti ali kuti.

Ngakhale mwanayu ali ndi ulumali ndipo amafunika chisamaliro chochuluka pafupifupi, mai ake amamutsekera mnyumba akamapita kochita malonda awo a tomato.

”Ndimakakamizika kumutsekera mnyumba ndi cholinga choti ndikagulitse malonda kuti ndipeze thandizo la chakudya komanso zinthu zina zofunika pa moyo wa tsiku ndi tsiku.

“Ndimachita izi kaamba koti palibe wina amene angamusamalire komanso azibale ake ena ndi achichepele,” adatero mai Lobeni.

Pakadali pano, mai Lobeni ati akupempha anthu akufuna kwabwino kuti awathandize ndi njinga ya anthu a ulumali  kuti mavuto omwe mwana wawo akukumana nalo mwina angachepe.

Iwo adawonjezeranso kupempha akufuna kwabwino kuti awathandize ndi mpamba wa bizinezi kuti ayambe kuchita geni yolozeka komanso kuti azitha kukhala ndi nthawi yochuluka yosamalira mwana wawo.

Follow us on Twitter:

Advertisement