Mwambo wodzodza ma Deacon 20 ampingo wa Katolika udachitika Loweruka ku St Peters Major Seminary mu Diocese ya Zomba ndipo adatsogolera mwambowo ndi Bishop wothandidzira mu Diocese ya Chipata Mdziko la Zambia Ambuye Gabriel Msipu Phiri.
Poyankhula pamwambowo, Bishop Msipu Phiri adati kudzodzedwa kwa ma Deacon atsopanowo kupangitsa kuti mdziko la Malawi mudzakhale ansembe ochuluka mtsogolo muno. Pamenepa adathokoza ma Deacon atsopanowo chifukwa chovomera kuyitana kwa Mulungu ndipo adawalimbikitsa kuti adziyika Mulungu patsolo nthawi zonse komanso asamataye mtima ngati akukumana ndi zovuta.
Iwo adalangizanso ma Deacon omwe adzodzedwa kumenewo kuti adzipempha nzeru kwa ansembe awo ndipo akhale odzichepetsa pakati atsogoleri awo.
Bishop Gabriel Msipu Phiri adathokoza Bungwe lama Episkopi akuno ku Malawi la Episcopal Conference of Malawi (ECM) chifukwa chowavomera kudzatsogolera mwambowo mdziko muno.
Iwo adathokozanso makolo chifukwa chovemera ana awo kutsata njira yotumikira Mulungu ndipo adapempha akhristu kuti atengepo mbali yothandiza achinyamata omwe akufuna kutsata njira ya Mulungu.
“Ndithokoze ansembe omwe amatsula anyamata kuti akhale ansembe ndipo ife ma Bishop timadziwa kuti mumakumana ndi mamvuto osiyana siyana koma Mulungu yekha ndiyemwe arzikudalitsani,” adatero Bishop Gabriel Msipu Phiri.
Mu mau ake, Deacon George Nambazo ochokera ku Holy Trinity Matawale Parish mu Diocese ya Zomba adathokoza Mulungu chifukwa chazadzikulu zimene wamuchitira.
Iye wathokozanso makolo ake chifukwa chomuphunzitsa komanso chomulimbikitsa kuti atumikire Mulungu.
Pamenepa Deacon Nambazo adapempha akhristu kuti adzimupemphelera kuti khumbo lake alikwaniritse lofuna kudzakhala Wansembe.
Follow us on Twitter: